Salimo 80:1-19

Kwa wotsogolera nyimbo pa Maluwa.*+ Chikumbutso.* Nyimbo ndi Salimo la Asafu.+ 80  Inu M’busa wa Isiraeli, tcherani khutu,+Inu amene mukutsogolera Yosefe ngati gulu la nkhosa.+Inu amene mwakhala pa akerubi,+ walani.+   Sonyezani mphamvu zanu pa Efuraimu, Benjamini ndi Manase,+Ndipo bwerani mudzatipulumutse.+   Inu Mulungu, tibwezeretseni mwakale.+Walitsani nkhope yanu kuti tipulumutsidwe.+   Inu Yehova Mulungu wa makamu, mudzakwiyira mapemphero a anthu anu mpaka liti?+   Mwawapatsa misozi kuti ikhale chakudya chawo,+Ndipo mukuwamwetsabe misozi yochuluka kwambiri.+   Mwachititsa kuti anthu oyandikana nafe azimenyana polimbirana ifeyo.+Ndipo adani athu akupitirizabe kutinyoza mmene akufunira.+   Inu Mulungu wa makamu, tibwezeretseni mwakale.+Walitsani nkhope yanu kuti tipulumutsidwe.+   Munachititsa mtengo wa mpesa kuchoka mu Iguputo.+Munapitikitsa mitundu ya anthu kuti mubzalemo mtengowo.+   Munalambula malo obzalapo mtengo wa mpesawo+ kuti uzike mizu ndi kudzaza dziko.+ 10  Mapiri anaphimbika ndi mthunzi wake,Ndipo mikungudza ya Mulungu inaphimbika ndi nthambi zake.+ 11  Pang’onopang’ono nthambi zake zinafika kunyanja,+Ndipo mphukira zake zinafika ku Mtsinje.*+ 12  N’chifukwa chiyani mwagwetsa mpanda wake wamiyala?+Ndipo n’chifukwa chiyani anthu onse odutsa mumsewu akuthyola zipatso zake?+ 13  Nguluwe ikuwononga mtengowo,+Ndipo magulu a nyama zakutchire akuudya.+ 14  Inu Mulungu wa makamu, chonde bwererani.+Yang’anani pansi pano muli kumwambako, ndipo onani ndi kusamalira mtengo wa mpesa uwu.+ 15  Onani muzu umene dzanja lanu lamanja linabzala.+Muonenso mwana wanu amene munamulimbitsa kuti inu mulemekezeke.+ 16  Watenthedwa ndi moto ndi kudulidwa.+Iwo amawonongeka ndi kudzudzula kwa pankhope panu.+ 17  Dzanja lanu likhale pa munthu wa kudzanja lanu lamanja,+Ndipo likhale pa mwana wa munthu amene mwamulimbitsa kuti mulemekezeke.+ 18  Ndipo ife sitidzabwerera kukusiyani.+Tisungeni amoyo kuti tiitane pa dzina lanu.+ 19  Inu Yehova Mulungu wa makamu, tibwezeretseni mwakale.+Walitsani nkhope yanu kuti tipulumutsidwe.+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Sl 45:Kamutu.
Onani Sl 60:Kamutu.
Umenewu ndi mtsinje wa Firate.