Salimo 53:1-6
Kwa wotsogolera nyimbo pa Mahalati.*+ Masikili.* Salimo la Davide.
53 Wopusa amanena mumtima mwake kuti:“Kulibe Yehova.”+Anthu oterewa amachita zoipa, ndipo amachita zinthu zonyansa zogwirizana ndi kupanda chilungamo kwawo.+Palibe amene akuchita zabwino.+
2 Koma kuchokera kumwamba, Mulungu wayang’ana ana a anthu padziko lapansi,+Kuti aone ngati pali aliyense wozindikira, aliyense amene akufunafuna Yehova.+
3 Onse abwerera, ndipo onsewo ndi achinyengo.+Palibe aliyense amene akuchita zabwino,+Palibiretu ndi mmodzi yemwe.
4 Kodi palibe aliyense wozindikira mwa anthu ochita zopweteka anzawowa,+Amene akudya anthu anga ngati chakudya?+Iwo sanaitane pa Yehova.+
5 Nthawi yomweyo anagwidwa ndi mantha aakulu,+Ngakhale kuti panalibe chochititsa mantha.+Pakuti Mulungu adzamwaza mafupa a aliyense womanga msasa kuti akuukireni.+Isiraeli adzawachititsa manyazi pakuti Yehova wawakana.+
6 Haa! Zikanakhala bwino m’Ziyoni mukanapezeka chipulumutso cha Isiraeli.+Yehova akadzasonkhanitsa ndi kubwezeretsa anthu ake amene agwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina,+Yakobo adzasangalale, Isiraeli adzakondwere.+
Mawu a M'munsi
^ “Mahalati” ndi mawu achiheberi. N’kutheka kuti ndi mawu okhudzana ndi nyimbo, mwina okhudzana ndi luso la kaimbidwe.