Salimo 147:1-20
147 Tamandani Ya, anthu inu,+Pakuti kuimbira Mulungu wathu nyimbo zomutamanda n’kwabwino,+Ndipo n’kosangalatsa. Kumutamanda n’koyenera.+
2 Yehova akumanga Yerusalemu.+Anthu okhala mu Isiraeli amene anabalalika akuwasonkhanitsanso pamodzi.+
3 Iye amachiritsa+ anthu osweka mtima,+Ndipo amamanga zilonda zawo zopweteka.+
4 Amawerenga nyenyezi zonse,+Ndipo zonsezo amazitchula mayina ake.+
5 Ambuye wathu ndi wamkulu ndipo ali ndi mphamvu zochuluka.+Nzeru zake zilibe malire.+
6 Yehova amathandiza anthu ofatsa,+Koma anthu oipa amawagwetsera pansi.+
7 Imbirani Yehova molandizana mawu nyimbo zomuyamikira anthu inu.+Imbirani Mulungu wathu nyimbo zomutamanda ndi zeze.+
8 Muimbireni Iye amene amaphimba mapiri ndi mitambo,+Amene amakonza mvula kuti igwe padziko lapansi,+Amenenso amameretsa udzu wobiriwira m’mapiri.+
9 Iye amapatsa zilombo chakudya chawo,+Amapatsanso ana a makwangwala chakudya chimene amalirira.+
10 Iye sadalira mphamvu za hatchi,+Kapena liwiro la miyendo ya munthu.+
11 Yehova amasangalala ndi anthu amene amamuopa,+Amene amayembekezera kukoma mtima kwake kosatha.+
12 Yamika Yehova,+ iwe Yerusalemu.Tamanda Mulungu wako, iwe Ziyoni.+
13 Pakuti walimbitsa mipiringidzo ya zipata zako.Wadalitsa ana ako amene ali mwa iwe.+
14 Iye akukhazikitsa mtendere m’dziko lako.+Ndipo akupitirizabe kukukhutiritsa ndi tirigu wabwino koposa.+
15 Amatumiza mawu ake padziko lapansi,+Ndipo mawu akewo amathamanga kwambiri.
16 Iye amapereka chipale chofewa kuti chikhale ngati ubweya wa nkhosa.+Amamwaza mame oundana ngati kuti ndi phulusa.+
17 Amaponya madzi oundana ngati nyenyeswa za chakudya.+Ndani angaime m’chisanu chake?+
18 Amatumiza mawu ake+ ndi kusungunula madzi oundanawo.Amachititsa mphepo yake kuwomba,+Ndipo madzi amayenda.
19 Amauza Yakobo mawu ake,+Ndipo amauza Isiraeli malangizo+ ake ndi zigamulo zake.+
20 Sanachite zimenezi ndi mtundu wina uliwonse,+Ndipo mitundu inayo sikudziwa zigamulo zake.+Tamandani Ya, anthu inu!+