Salimo 47:1-9

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ndi Salimo la ana a Kora. 47  Ombani m’manja anthu nonsenu.+Fuulirani Mulungu mokondwera chifukwa chakuti wapambana.+   Pakuti Yehova, Wam’mwambamwamba, ndi wochititsa mantha,+Ndiye Mfumu yaikulu padziko lonse lapansi.+   Iye adzagonjetsa mitundu ya anthu ndi kuiika pansi pathu.+Adzagonjetsa anthu a mitundu ina ndi kuwaika pansi pa mapazi athu.+   Adzatisankhira cholowa,+Chimene Yakobo, amene amamukonda, anakondwera nacho.+ [Seʹlah.]   Mulungu wakwera kumalo ake, anthu akufuula mokondwera,+Yehova wakwera kumalo ake, anthu akuliza lipenga la nyanga ya nkhosa.+   Imbani nyimbo zotamanda Mulungu, imbani nyimbo zotamanda.+Imbani nyimbo zotamanda Mfumu yathu, imbani nyimbo zotamanda.   Pakuti Mulungu ndi Mfumu ya dziko lonse lapansi.+Imbani nyimbo zotamanda ndi kuchita zinthu mozindikira.+   Mulungu wakhala mfumu ya mitundu ya anthu.+Mulungu wakhala pampando wake wachifumu wopatulika.+   Atsogoleri a mitundu ya anthu asonkhana.+Asonkhana pamodzi ndi anthu a Mulungu wa Abulahamu.+Pakuti anthu onse omwe ali ngati zishango* za dziko lapansi ndi a Mulungu.+Iye wakwera pamalo okwezeka kwambiri.+

Mawu a M'munsi

N’kutheka kuti mawu akuti “zishango” akunena olamulira kapena oteteza anthu.