Salimo 2:1-12

2  N’chifukwa chiyani anthu a mitundu ina akuchita chipolowe,+Ndiponso n’chifukwa chiyani mitundu ya anthu ikung’ung’udza za chinthu chopanda pake?+   Mafumu a dziko lapansi aima pamalo awo,+Ndipo nduna zapamwamba zasonkhana pamodzi mogwirizana.+Atero kuti alimbane ndi Yehova+ komanso wodzozedwa wake.+   Iwo akunena kuti: “Tiyeni tidule zomangira zawo,+Ndipo titaye zingwe zawo kutali ndi ife!”+   Iye wokhala kumwamba+ adzaseka,Yehova adzawanyodola.+   Pa nthawiyo, adzawalankhula mu mkwiyo wake,+Adzawasokoneza ataipidwa kwambiri.+   Ndipo adzanena kuti: “Inetu ndakhazika mfumu yanga+Pa Ziyoni,+ phiri langa lopatulika.”+   Ndinene za lamulo la Yehova.Iye wandiuza kuti: “Iwe ndiwe mwana wanga,+Lero, ine ndakhala bambo ako.+   Tandipempha,+ ndipo ndikupatsa mitundu ya anthu kukhala cholowa chako,+Ndikupatsa dziko lonse lapansi kukhala lako.+   Mitunduyo udzaiswa ndi ndodo yachifumu yachitsulo,+Udzaiphwanya ngati mbiya yadothi, n’kukhala zidutswazidutswa.”+ 10  Tsopano inu mafumu, sonyezani kuzindikira,Lolani kuti maganizo anu akonzedwe, inu oweruza a dziko lapansi.+ 11  Tumikirani Yehova mwamantha.+Kondwerani ndipo nthunthumirani.+ 12  Psompsonani mwanayo+ kuopera kuti Mulungu angakwiye,Ndipo mungawonongeke ndi kuchotsedwa panjirayo.+Pakuti mkwiyo wake umatha kuyaka mofulumira.+Odala ndi onse amene akuthawira kwa iye.+

Mawu a M'munsi