Salimo 118:1-29
118 Yamikani Yehova anthu inu, pakuti iye ndi wabwino.+Kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+
2 Tsopano Isiraeli anene kuti:“Kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.”+
3 A nyumba ya Aroni anene kuti:+“Kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.”+
4 Oopa Yehova anene kuti:+“Kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.”+
5 M’masautso anga ndinaitana Ya.+Ya anandiyankha ndi kundiika pamalo otakasuka.+
6 Yehova ali kumbali yanga, sindidzaopa.+Munthu wochokera kufumbi angandichite chiyani?+
7 Yehova ali kumbali yanga pamodzi ndi anthu amene akundithandiza,+Ndipo ine ndidzayang’ana anthu odana nane atagonja.+
8 Kuthawira kwa Yehova n’kwabwino+Kusiyana ndi kudalira munthu wochokera kufumbi.+
9 Kuthawira kwa Yehova n’kwabwino+Kusiyana ndi kudalira anthu olemekezeka.+
10 Mitundu yonse ya anthu inandizungulira,+Koma ndinali kuikankhira kutali m’dzina la Yehova.+
11 Mitunduyo inandizungulira, ndithu inandizungulira kumbali zonse.+Koma ndinali kuikankhira kutali m’dzina la Yehova.
12 Inandizungulira ngati njuchi,+Koma inazima ngati moto wa zitsamba zaminga.+Ndinali kuikankhira kutali m’dzina la Yehova.+
13 Munandikankha kwambiri kuti ndigwe,+Koma Yehova anandithandiza.+
14 Ya ndiye malo anga obisalapo ndi mphamvu zanga,+Iye amandipulumutsa.+
15 M’mahema+ a olungama+Mumamveka mfuu yachisangalalo ndipo muli chipulumutso.+Dzanja lamanja la Yehova limachita zamphamvu.+
16 Dzanja lamanja la Yehova likudzikweza pamwamba.+Dzanja lamanja la Yehova limachita zamphamvu.+
17 Sindidzafa, koma ndidzakhalabe ndi moyo,+Kuti ndilengeze ntchito za Ya.+
18 Ya anandilanga mwamphamvu,+Koma sanandipereke ku imfa.+
19 Nditsegulireni zipata zachilungamo,+ anthu inu.Ndidzalowamo ndipo ndidzatamanda Ya.+
20 Ichi ndi chipata cha Yehova.+Olungama adzalowamo.+
21 Ndidzakutamandani, chifukwa munandiyankha+Ndi kundipulumutsa.+
22 Mwala umene omanga nyumba anaukana+Wakhala mwala wofunika kwambiri wapakona.+
23 Umenewu wachokera kwa Yehova,+Ndipo ndi wodabwitsa m’maso mwathu.+
24 Ili ndi tsiku limene Yehova wapanga.+Tidzakondwera ndi kusangalala pa tsiku limeneli.+
25 Haa! Inu Yehova, chonde tipulumutseni.+Haa! Inu Yehova, chonde tithandizeni kuti zinthu zitiyendere bwino.+
26 Wodala ndi Iye wobwera m’dzina la Yehova.+Takudalitsani anthu inu potuluka m’nyumba ya Yehova.+
27 Yehova ndiye Mulungu,+Ndipo amatipatsa kuwala.+Kongoletsani gulu la anthu amene ali pachikondwerero+ ndi nthambi za mitengo,+ anthu inu.Likongoletseni mpaka kukafika panyanga za guwa lansembe.+
28 Inu ndinu Mulungu wanga, ndipo ndidzakutamandani.+Ndinu Mulungu wanga, ndipo ndidzakukwezani.+
29 Yamikani Yehova anthu inu, pakuti iye ndi wabwino.+Kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+