Salimo 39:1-13

Kwa wotsogolera nyimbo pa Yedutuni.*+ Nyimbo ya Davide. 39  Ine ndinati: “Ndidzatchinjiriza njira zanga,+Kuti ndisachimwe ndi lilime langa.+Ndidzamanga pakamwa panga kuti patetezeke,+Nthawi zonse pamene woipa ali pamaso panga.”+  2  Ndinakhala chete osalankhula kanthu.+Ndinakhala phee osanena ngakhale zinthu zabwino,+Ndipo ndinanyalanyaza ululu wanga.  3  Mumtima mwanga munatentha moto.+Pamene ndinali kuusa moyo, moto unali kuyakabe.Choncho ndinati:  4  “Inu Yehova, ndidziwitseni za kufulumira kwa chimaliziro changa,+Ndiponso kuti masiku anga ndi ochepa motani,+Kuti ndidziwe kufupika kwa moyo wanga.+  5  Taonani! Mwachepetsa masiku anga.+Ndipo nthawi ya moyo wanga si kanthu pamaso panu.+Ndithudi, munthu aliyense ngakhale atakhala wamphamvu bwanji, sali kanthu koma ali ngati mpweya wotuluka m’mphuno.+ [Seʹlah.]  6  Zoonadi, munthu amayenda ngati chithunzithunzi.+Ndithudi, anthu amapokosera pachabe.+Munthu amaunjika zinthu ndipo sadziwa amene adzazitute.+  7  Nanga tsopano, inu Yehova, ine ndikuyembekezera chiyani?Chiyembekezo changa chili mwa inu.+  8  Ndilanditseni ku zolakwa zanga zonse.+Musalole kuti munthu wopusa azinditonza.+  9  Ndinakhala chete.+ Sindinatsegule pakamwa panga,+Pakuti inu munachitapo kanthu.+ 10  Ndichotsereni mliri umene mwandigwetsera.+Ine ndatha chifukwa cha ukali wa dzanja lanu.+ 11  Mwa kudzudzula cholakwa, mwawongolera munthu,+Ndipo mwawononga zinthu zake zamtengo wapatali ngati mmene njenjete*+ imachitira.Ndithudi, munthu aliyense ali ngati mpweya.+ [Seʹlah.] 12  Imvani pemphero langa, inu Yehova,Ndipo tcherani khutu pamene ndikufuula kupempha thandizo.+Musandinyalanyaze pamene ndikugwetsa misozi.+Pakuti ndine mlendo wanu,+Mlendo wokhala nanu monga anachitira makolo anga onse.+ 13  Musandiyang’ane mutakwiya, kuti ndikhalenso wosangalala+Ndisanamwalire ndi kuiwalika.”+

Mawu a M'munsi

^ “Yedutuni” ndi mawu achiheberi amene tanthauzo lake silikudziwika.
^ Mawu achiheberi amene tawamasulira kuti “njenjete” amatanthauza mtundu wa kachilombo kotchedwa kadziwotche kooneka ngati gulugufe, kamene kamadya zovala ngati mmene njenjete imachitira.