Salimo 54:1-7

Kwa wotsogolera nyimbo: Nyimboyi iimbidwe ndi zipangizo za zingwe. Masikili.* Salimo la Davide. Pa nthawi imene Zifi anabwera kudzauza Sauli kuti: “Kodi simukudziwa kuti Davide akubisala kwathu?”+ 54  Inu Mulungu, ndipulumutseni m’dzina lanu,+Ndipo ndithandizeni ndi mphamvu zanu.+   Inu Mulungu, imvani pemphero langa.+Tcherani khutu ku mawu ochokera m’kamwa mwanga.+   Pakuti pali anthu achilendo amene andiukira,Ndipo pali olamulira ankhanza amene akufuna moyo wanga.+Sanaike Mulungu patsogolo pawo.+ [Seʹlah.]   Taonani! Mulungu ndiye mthandizi wanga.+Yehova ali pakati pa anthu amene akuchirikiza moyo wanga.   Iye adzabwezera zoipa kwa adani anga.+Achititseni kukhala chete chifukwa cha choonadi chanu.+   Ndidzapereka nsembe kwa inu mofunitsitsa.+Inu Yehova, ndidzatamanda dzina lanu pakuti ndi labwino.+   Pakuti anandilanditsa pa mavuto anga onse,+Ndipo diso langa laona adani anga atagonja.+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Sl 32:Kamutu.