Salimo 11:1-7
Kwa wotsogolera nyimbo. Salimo la Davide.
11 Ine ndathawira kwa Yehova.+Kodi mulibe mantha? Mukundiuza kuti:“Thawirani kumapiri anu ngati mbalame!+
2 Pakuti oipa akunga uta,+Akonzekeretsa mivi yawo kuti aiponye ndi uta,Kuti alase anthu owongoka mtima kuchokera pamalo amdima.+
3 Kodi munthu wolungama angachite chiyaniMaziko achilungamo atagumulidwa?”+
4 Yehova ali m’kachisi wake wopatulika.+Yehova, mpando wake wachifumu uli kumwamba.+Maso ake amaona, maso ake owala amasanthula+ ana a anthu.
5 Yehova amasanthula anthu olungama ndi oipa omwe,+Ndipo Mulungu amadana kwambiri ndi aliyense wokonda chiwawa.+
6 Iye adzavumbitsira oipa misampha, moto ndi sulufule,+Komanso mphepo yotentha, monga gawo limene ayenera kumwa.+
7 Pakuti Yehova ndi wolungama.+ Amakonda ntchito zolungama.+Anthu owongoka mtima ndi amene adzaona nkhope yake.+