Salimo 150:1-6

150  Tamandani Ya, anthu inu!+Tamandani Mulungu m’malo ake oyera.+Mutamandeni m’mlengalenga mmene mumasonyeza mphamvu zake.+   Mutamandeni chifukwa cha ntchito zake zamphamvu.+Mutamandeni mogwirizana ndi ukulu wake wosaneneka.+   Mutamandeni mwa kuliza lipenga la nyanga ya nkhosa.+Mutamandeni ndi choimbira cha zingwe ndi zeze.+   Mutamandeni ndi maseche+ ndi gule wovina mozungulira.+Mutamandeni ndi zoimbira za zingwe+ ndi chitoliro.+   Mutamandeni ndi chinganga cha mawu osangalatsa.+Mutamandeni ndi chinganga cha mawu amphamvu.+   Chopuma chilichonse chitamande Ya.+Tamandani Ya, anthu inu!+

Mawu a M'munsi