Salimo 82:1-8
Nyimbo ya Asafu.
82 Mulungu waima pakati pa msonkhano wake,+Ndipo akuweruza pakati pa milungu kuti:+
2 “Kodi mudzaweruza mopanda chilungamo,+Ndi kukondera anthu oipa kufikira liti?+ [Seʹlah.]
3 Chitirani chilungamo anthu onyozeka ndi ana amasiye.*+Chitirani chilungamo anthu osautsika ndi osauka.+
4 Pulumutsani munthu wonyozeka ndi wosauka.+Alanditseni m’manja mwa anthu oipa.”+
5 Milunguyo siikudziwa kanthu ndipo siikuzindikira.+Ikuyendayenda mu mdima,+Ndipo maziko onse a dziko lapansi agwedezeka.+
6 “Ine ndanena kuti, ‘Inu ndinu milungu,+Ndipo nonsenu ndinu ana a Wam’mwambamwamba.+
7 Ndithudi, mudzafa mmene anthu onse amafera.+Ndipo mudzagwa mmene kalonga aliyense amagwera!’”+
8 Nyamukani inu Mulungu, weruzani dziko lapansi.+Pakuti inu nokha muyenera kutenga mitundu yonse kukhala yanu.+
Mawu a M'munsi
^ Mawu ake enieni, “ana aamuna opanda bambo.”