Salimo 82:1-8
Nyimbo ya Asafu.+
82 Mulungu waima pamsonkhano wake,*+Akuweruza pakati pa milungu* kuti:+
2 “Kodi mupitiriza kuweruza mopanda chilungamo+Komanso kukondera anthu oipa mpaka liti?+ (Selah)
3 Tetezani* anthu onyozeka ndi ana amasiye.+
Chitirani chilungamo anthu amene alibe wowathandiza komanso osauka.+
4 Pulumutsani munthu wonyozeka ndi wosauka.Alanditseni mʼmanja mwa anthu oipa.”
5 Milunguyo sikudziwa kapena kuzindikira.+Ikuyendayenda mumdima,Maziko onse a dziko lapansi agwedezeka.+
6 “Ine ndanena kuti, ‘Inu ndinu milungu,*+Nonsenu ndinu ana a Wamʼmwambamwamba.
7 Koma mudzafa ngati mmene anthu onse amafera.+Ndipo mudzagwa ngati mmene kalonga aliyense amagwera!’”+
8 Nyamukani inu Mulungu, ndipo muweruze dziko lapansi,+Chifukwa mitundu yonse ya anthu ndi yanu.
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “pamsonkhano wa Mulungu.”
^ Kapena kuti, “pakati pa ofanana ndi mulungu.”
^ Kapena kuti, “Weruzani.”
^ Kapena kuti, “ofanana ndi mulungu.”