Salimo 19:1-14
Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ya Davide.
19 Zinthu zakumwamba zikulengeza ulemerero wa Mulungu.+Ndipo mumlengalenga mukufotokoza ntchito ya manja ake.+
2 Tsiku lililonse, mawu awo amamveka,Ndipo usiku uliwonse zimasonyeza nzeru zake.
3 Sizilankhula kapena kutulutsa mawu.Mawu awo samveka.
4 Koma mawu awo amveka* padziko lonse lapansi,Ndipo uthenga wawo wamveka kumalekezero a dziko lapansi kumene kuli anthu.+
Mulungu wamangira dzuwa tenti kumwamba.
5 Dzuwalo limaoneka ngati mkwati amene akutuluka mʼchipinda chake,Limasangalala ngati mwamuna wamphamvu amene akuthamanga pampikisano.
6 Limatuluka kuchokera kumalekezero ena akumwamba,Nʼkuzungulira mpaka kumalekezero enanso.+Ndipo palibe chilichonse chimene sichimva kutentha kwake.
7 Chilamulo cha Yehova ndi changwiro,+ chimabwezeretsa mphamvu.*+
Zikumbutso za Yehova ndi zodalirika,+ zimapatsa nzeru munthu wosadziwa zinthu.+
8 Malamulo ochokera kwa Yehova ndi olungama, amasangalatsa mtima.+Chilamulo cha Yehova ndi choyera, chimatsegula maso.+
9 Kuopa Yehova+ nʼkoyera, ndipo kudzakhalapo kwamuyaya.
Zigamulo za Yehova nʼzolondola, ndipo pa mbali iliyonse ndi zolungama.+
10 Nʼzosilirika kuposa golide,Kuposa golide wambiri woyengeka bwino.+Ndipo nʼzotsekemera kuposa uchi,+ kuposa uchi umene ukukha mʼzisa.
11 Ndiponso mtumiki wanu amachenjezedwa nazo.+Munthu wosunga zigamulozo amapeza mphoto yaikulu.+
12 Ndi ndani amene angazindikire yekha zinthu zimene walakwitsa?+
Mundikhululukire machimo amene ndachita mosadziwa.
13 Ndipo mundiletse kuchita zinthu modzikuza, ine mtumiki wanu.+Musalole kuti kudzikuza kundilamulire.+
Mukatero ndidzakhala wopanda chifukwa,+Komanso ndidzakhala wopanda mlandu wa machimo akuluakulu.*
14 Mawu apakamwa panga komanso zimene ndimaganizira mozama mumtima mwanga,Zizikusangalatsani, inu Yehova,+ Thanthwe langa+ ndiponso Wondiwombola.+
Mawu a M'munsi
^ Mabaibulo ena amati, “muyeso wawo wamveka.”
^ Kapena kuti, “chimabwezeretsa moyo.”
^ Kapena kuti, “wa zolakwa zambiri.”