Salimo 106:1-48

 • Aisiraeli sanasonyeze kuyamikira

  • Anaiwala mwamsanga zimene Mulungu anachita (13)

  • Anasinthanitsa ulemerero wa Mulungu ndi chifaniziro cha mwana wangʼombe (19, 20)

  • Sankakhulupirira malonjezo a Mulungu (24)

  • Anayamba kulambira Baala (28)

  • Ankapereka nsembe ana awo kwa ziwanda (37)

106  Tamandani Ya!* Yamikani Yehova chifukwa iye ndi wabwino.+Chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.+   Ndi ndani amene anganene za ntchito zonse zazikulu za Yehova,Kapena kulengeza zochita zake zonse zotamandika?+   Osangalala ndi anthu amene amachita zinthu mwachilungamo,Amene amachita zinthu zolungama nthawi zonse.+   Ndikumbukireni inu Yehova, pamene mukusonyeza anthu anu kukoma mtima.+ Ndisamalireni ndi kundipulumutsa,   Kuti ndisangalale ndi ubwino umene mumasonyeza osankhidwa anu,+Kuti ndikondwere limodzi ndi mtundu wanu,Ndiponso kuti ndikutamandeni monyadira pamodzi ndi cholowa chanu.   Tachimwa mofanana ndi makolo athu.+Tachita zinthu zolakwika, tachita zinthu zoipa.+   Makolo athu ku Iguputo, sanayamikire* ntchito zanu zodabwitsa. Sanakumbukire chikondi chanu chokhulupirika chomwe ndi chochuluka,Koma anapanduka panyanja, pafupi ndi Nyanja Yofiira.+   Koma Mulungu anawapulumutsa kuti dzina lake lilemekezedwe,+Kuti mphamvu zake zidziwike.+   Iye analamula* ndipo Nyanja Yofiira inauma.Anatsogolera anthu ake kudutsa pakati pa madzi akuya ngati akudutsa mʼchipululu.+ 10  Anawapulumutsa mʼmanja mwa anthu amene ankadana nawo+Ndipo anawawombola mʼmanja mwa mdani.+ 11  Madzi anamiza adani awo,Moti panalibe ngakhale mmodzi amene anapulumuka.*+ 12  Zitatero anakhulupirira zimene anawalonjeza.+Anayamba kumuimbira nyimbo zomutamanda.+ 13  Koma mofulumira anaiwala zimene Mulungu anachita.+Sanadikire kuti Mulungu awapatse malangizo. 14  Iwo anasonyeza mtima wadyera mʼchipululu,+Ndipo anayesa Mulungu mʼchipululumo.+ 15  Mulungu anawapatsa zimene anapempha,Koma anawagwetsera matenda amene anawachititsa kuti awonde kwambiri.+ 16  Mumsasa, iwo anayamba kuchitira nsanje MoseNdiponso Aroni,+ woyera wa Yehova.+ 17  Kenako dziko lapansi linatseguka ndipo linameza Datani,Nʼkukwirira anthu onse amene anali kumbali ya Abiramu.+ 18  Moto unayaka pakati pa gulu lawo.Malawi amoto anapsereza oipa.+ 19  Iwo anapanga mwana wa ngʼombe ku Horebe,Ndipo anagwadira fano lachitsulo.*+ 20  Anasinthanitsa ulemerero wangaNdi chifaniziro cha ngʼombe yamphongo yodya udzu.+ 21  Iwo anaiwala Mulungu,+ Mpulumutsi wawo,Amene anachita zinthu zazikulu ku Iguputo,+ 22  Amene anachita zodabwitsa mʼdziko la Hamu,+Amene anachita zochititsa mantha pa Nyanja Yofiira.+ 23  Iye anangotsala pangʼono kulamula kuti awonongedwe,Koma Mose wosankhidwa wake, anamuchonderera*Kuti asawagwetsere mkwiyo wake wowononga.+ 24  Pa nthawiyo iwo ananyoza dziko losiririka,+Ndipo analibe chikhulupiriro pa zimene anawalonjeza.+ 25  Anapitiriza kungʼungʼudza mʼmatenti awo.+Iwo sanamvere mawu a Yehova.+ 26  Choncho Mulungu anawalumbirira atakweza dzanja lake,Kuti adzachititsa kuti afere mʼchipululu.+ 27  Adzachititsa kuti mbadwa zawo ziphedwe ndi anthu a mitundu ina,Ndiponso kuwamwaza mʼmayiko osiyanasiyana.+ 28  Kenako iwo anayamba kulambira* Baala wa ku Peori,+Ndipo anadya nsembe zoperekedwa kwa akufa.* 29  Iwo anamukwiyitsa chifukwa cha zochita zawo,+Ndipo pakati pawo panagwa mliri.+ 30  Koma Pinihasi ataimirira nʼkuchitapo kanthu,Mliriwo unatha.+ 31  Ndipo Pinihasi ankaonedwa kuti ndi wolungamaKu mibadwo yonse mpaka kalekale.+ 32  Iwo anamukwiyitsanso pa madzi a ku Meriba,*Moti Mose sizinamuyendere bwino chifukwa cha anthu amenewa.+ 33  Iwo anamukwiyitsaNdipo Mose analankhula mosaganiza bwino.+ 34  Iwowa sanawononge mitundu ina ya anthu,+Ngati mmene Yehova anawalamulira.+ 35  Koma anayamba kusakanikirana ndi anthu a mitundu ina,+Nʼkuyamba* kuchita zinthu ngati mmene iwo ankachitira.+ 36  Ankatumikira mafano awo,+Ndipo mafanowo anakhala msampha kwa iwo.+ 37  Ankapereka nsembe ana awo aamunaKomanso ana awo aakazi kwa ziwanda.+ 38  Ankakhetsa magazi a anthu osalakwa,+Magazi a ana awo aamuna komanso a ana awo aakazi,Amene anawapereka nsembe kwa mafano a ku Kanani.+Ndipo dzikolo linaipa ndi magazi amene iwo anakhetsa. 39  Iwo anakhala odetsedwa chifukwa cha ntchito zawo.Anachita uhule ndi milungu ina chifukwa cha zochita zawo.+ 40  Choncho mkwiyo wa Yehova unayakira anthu ake,Ndipo iye anayamba kunyansidwa ndi cholowa chake. 41  Mobwerezabwereza ankawapereka mʼmanja mwa anthu a mitundu ina,+Kuti anthu amene ankadana nawo aziwalamulira.+ 42  Adani awo ankawapondereza,Ndipo anali pansi pa ulamuliro wawo. 43  Nthawi zambiri ankawapulumutsa,+Koma iwo ankamupandukira komanso sankamvera,+Ndipo ankawonongedwa chifukwa cha zolakwa zawo.+ 44  Koma Mulungu ankaona mavuto amene akukumana nawo+Ndipo ankamva kulira kwawo kopempha thandizo.+ 45  Pofuna kuwathandiza iye ankakumbukira pangano lake,Ndipo ankawamvera chisoni* chifukwa cha chikondi chake chokhulupirika chomwe ndi chachikulu.*+ 46  Iye ankachititsa kuti anthu onse amene anawagwira ukapolo+Awamvere chisoni. 47  Tipulumutseni inu Yehova Mulungu wathu,+Ndi kutisonkhanitsa pamodzi kuchokera mʼmitundu ina,+Kuti titamande dzina lanu loyera,Komanso kuti tikutamandeni mosangalala.+ 48  Atamandike Yehova, Mulungu wa Isiraeli,Mpaka kalekale.*+ Ndipo anthu onse anene kuti, “Ame!” Tamandani Ya,*

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Aleluya.” “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.
Kapena kuti, “sanamvetse tanthauzo la.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “anadzudzula.”
Kapena kuti, “amene anatsala.”
Kapena kuti, “anagwadira chitsulo chosungunula.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “anaima pamalo ogumuka pamaso pa Mulungu.”
Kapena kuti, “kudzipereka kwa.”
Zimenezi ndi nsembe zimene mwina ankapereka kwa anthu akufa kapena milungu yopanda moyo.
Kutanthauza, “Kukangana.”
Kapena kuti, “Nʼkuphunzira.”
Kapena kuti, “chochuluka.”
Kapena kuti, “Ndipo ankasintha maganizo.”
Kapena kuti, “Kuyambira kalekale mpaka kalekale.”
Kapena kuti, “Aleluya.” “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.