FUNSO 3
Kodi ndi Ndani Amene Analemba Baibulo?
“Mose analemba mawu onse a Yehova.”
“Danieli analota maloto ndipo anaona masomphenya atagona pabedi lake. Ndiyeno analemba zimene analotazo ndipo anafotokoza nkhani yonseyo.”
“Pamene munalandira mawu a Mulungu amene munamva kwa ife, simunawalandire monga mawu a anthu, koma mmene alilidi, monga mawu a Mulungu.”
“Malemba onse anauziridwa ndi Mulungu, ndipo ndi othandiza pophunzitsa.”
“Ulosi sunachokere kwa anthu, koma anthuwo analankhula mawu ochokera kwa Mulungu motsogoleredwa ndi mzimu woyera.”