Salimo 65:1-13

  • Mulungu amasamalira dziko lapansi

    • “Wakumva pemphero” (2)

    • ‘Wosangalala ndi munthu amene inu mwamusankha’ (4)

    • Mulungu ali ndi zinthu zambiri zabwino (11)

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ndi Salimo la Davide. 65  Inu Mulungu, tidzakutamandani mu Ziyoni,+Tidzakwaniritsa malonjezo athu kwa inu.+   Inu Wakumva pemphero, anthu a mitundu yonse adzabwera kwa inu.+   Zolakwa zanga zandikulira,+Koma inu mumatikhululukira machimo athu.+   Wosangalala ndi munthu amene inu mwamusankha nʼkumubweretsa pafupi ndi inu,Kuti akhale mʼmabwalo anu.+ Tidzakhutira ndi zinthu zabwino zamʼnyumba yanu,+Kachisi wanu woyera.*+   Mudzatiyankha pochita zinthu zachilungamo zomwe ndi zochititsa mantha,+Inu Mulungu amene mumatipulumutsa.Anthu amene amakhala kumbali zonse za dziko lapansi amakudalirani+Kuphatikizapo amene amakhala kutali, kutsidya la nyanja.   Ndi mphamvu zanu, munakhazikitsa mapiri mʼmalo ake,Inu muli ndi mphamvu zochuluka.+   Mumachititsa kuti nyanja imene ikuchita mafunde ikhale bata.+Mumaletsa phokoso la mafunde ake komanso chipwirikiti cha mitundu ya anthu.+   Anthu okhala mʼmadera akutali adzachita mantha ndi zizindikiro zanu.+Mudzachititsa kuti anthu amene amakhala kumene dzuwa limatulukira mpaka kumene limalowera afuule mosangalala.   Inu mumasamalira dziko lapansi,Mumalichititsa kuti libale zipatso zambiri* komanso kuti likhale lachonde.+ Mtsinje wochokera kwa Mulungu ndi wodzadza ndi madzi.Mumachititsa kuti dziko lapansi lipereke chakudya kwa anthu,+Umu ndi mmene dziko lapansi munalipangira. 10  Mumanyowetsa minda yake komanso kusalaza dothi limene lalimidwa,*Mumaifewetsa ndi mvula yamvumbi. Mumadalitsa zomera zake.+ 11  Chaka mumachiveka zinthu zabwino ndipo zimakhala ngati mwachiveka chisoti chachifumu.Munjira zanu mumakhala zinthu zambiri zabwino.*+ 12  Mʼmalo odyetserako ziweto amʼchipululu muli msipu wambiri.*+Ndipo zitunda zavekedwa chisangalalo.+ 13  Malo odyetserako ziweto adzaza ndi nkhosa,Ndipo mʼzigwa muli tirigu yekhayekha.+ Malo onsewa akufuula komanso kuimba mosangalala.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Malo oyera.”
Kapena kuti, “lisefukire ndi zokolola.”
Kapena kuti, “kusalaza mizere yake.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Njira zanu zimakha mafuta.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mukukha mafuta.”