Salimo 14:1-7
Kwa wotsogolera nyimbo. Salimo la Davide.
14 Munthu wopusa* amanena mumtima mwake kuti:
“Kulibe Yehova.”+
Zochita za anthu amenewa ndi zoipa komanso zonyansa,Ndipo palibe amene akuchita zabwino.+
2 Koma kuchokera kumwamba, Yehova amayangʼana ana a anthu,Kuti aone ngati pali aliyense wozindikira, ngati pali aliyense amene akufunafuna Yehova.+
3 Onse apatuka,+Ndipo onsewo ndi achinyengo.
Palibe aliyense amene akuchita zabwino,Palibiretu ndi mmodzi yemwe.
4 Kodi palibe aliyense womvetsa zinthu pakati pa anthu ochita zoipawa?
Iwo amadya anthu anga ngati kuti akudya chakudya.
Ndipo sapemphera kwa Yehova.
5 Koma adzagwidwa ndi mantha aakulu,+Chifukwa Yehova ali pakati pa mʼbadwo wa anthu olungama.
6 Inu anthu ochita zoipa mumayesetsa kusokoneza mapulani a munthu wonyozeka,Koma Yehova ndi malo ake othawirako.+
7 Zikanakhala bwino chipulumutso cha Isiraeli chikanachokera ku Ziyoni.+
Yehova akadzabwezeretsa anthu ake amene anagwidwa nʼkutengedwa kupita kudziko lina,Yakobo adzasangalale, Isiraeli adzakondwere.
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “wopanda nzeru.”