Salimo 40:1-17
Kwa wotsogolera nyimbo. Salimo la Davide.
40 Ndinayembekezera Yehova ndi mtima wonse,*Ndipo iye anatchera khutu* kwa ine nʼkumva kulira kwanga kopempha thandizo.+
2 Iye ananditulutsa mʼdzenje la madzi a mkokomo,Ananditulutsa mʼchithaphwi cha matope.
Ndipo anapondetsa phazi langa pathanthwe,Anachititsa kuti ndiyende panthaka yolimba.
3 Kenako anaika nyimbo yatsopano mʼkamwa mwanga,+Nyimbo yotamanda Mulungu wathu.
Ambiri adzaona zimenezi ndipo adzachita mantha,Nʼkuyamba kukhulupirira Yehova.
4 Wosangalala ndi munthu amene amakhulupirira YehovaKomanso amene sadalira anthu otsutsa kapena anthu amene amakhulupirira mabodza.*
5 Inu Yehova Mulungu wanga,Mwatichitira zinthu zambiri zodabwitsa+Ndipo mumatiganizira.+
Palibe angafanane ndi inu.Nditati ndilankhule kapena kunena za zodabwitsazo,Zingakhale zochuluka kwambiri moti sindingathe kuzifotokoza.+
6 Nsembe zanyama komanso nsembe zina, simunazifune.*+Koma munatsegula makutu anga kuti ndimve.+
Simunapemphe nsembe zopsereza ndi nsembe zamachimo.+
7 Ndiyeno ine ndinati: “Taonani, ine ndabwera.
Mumpukutu* munalembedwa za ine.+
8 Ndimasangalala* kuchita zimene mumafuna, inu Mulungu wanga,+Ndipo chilamulo chanu chili mumtima mwanga.+
9 Ndimalengeza uthenga wabwino wa chilungamo mumpingo waukulu.+
Onani! Sinditseka pakamwa panga,+Monga mmene mukudziwira, Inu Yehova.
10 Sindibisa chilungamo chanu mumtima mwanga.
Ndimalengeza kuti ndinu wokhulupirika komanso kuti mumapulumutsa atumiki anu.
Sindibisa chikondi chanu chokhulupirika komanso choonadi chanu mumpingo waukulu.”+
11 Inu Yehova, musasiye kundisonyeza chifundo.
Chikondi chanu chokhulupirika komanso choonadi chanu zizinditeteza nthawi zonse.+
12 Masoka amene andizungulira ndi ambiri moti sindingathe kuwawerenga.+
Zolakwa zanga ndi zochuluka moti sindikutha kuona kumene ndikulowera.+Zachuluka kwambiri kuposa tsitsi lakumutu kwanga,Ndipo ndataya mtima.
13 Mukhale wofunitsitsa kundipulumutsa, inu Yehova.+
Ndithandizeni mofulumira, inu Yehova.+
14 Onse amene akufuna kuchotsa moyo wangaAchititsidwe manyazi komanso anyozeke.
Amene akusangalala ndi tsoka langaAbwerere mwamanyazi.
15 Onse amene akunena kuti: “Eyaa! Eyaa!”
Achite mantha kwambiri chifukwa cha zinthu zochititsa manyazi zimene ziwachitikire.
16 Koma amene akufunafuna inu,+Akondwere ndi kusangalala chifukwa choti akudziwani.+
Amene amasangalala ndi njira imene mumapulumutsira anthu, nthawi zonse azinena kuti:
“Yehova alemekezeke.”+
17 Koma ine ndine munthu wovutika komanso wosauka.Yehova aone zimene zikundichitikira.
Inu ndi amene mumandithandiza komanso kundipulumutsa.+Inu Mulungu wanga, musachedwe.+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “moleza mtima.”
^ Kapena kuti, “Ndipo iye anawerama kuti amvetsere.”
^ Kapena kuti, “anthu amabodza.”
^ Kapena kuti, “simunasangalale nazo.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Mumpukutu wa buku.”
^ Kapena kuti, “Ndimafunitsitsa.”