Salimo 54:1-7

  • Pemphero lopempha kuthandizidwa pa nthawi youkiridwa ndi adani

    • “Mulungu ndi amene amandithandiza” (4)

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimboyi iimbidwe ndi zipangizo za zingwe. Masikili.* Salimo la Davide. Pa nthawi imene amuna a ku Zifi anabwera kudzauza Sauli kuti: “Davide akubisala kwathu.”+ 54  Inu Mulungu, ndipulumutseni mʼdzina lanu,+Ndipo nditetezeni*+ ndi mphamvu zanu.   Inu Mulungu, imvani pemphero langa.+Tcherani khutu ku mawu ochokera mʼkamwa mwanga.   Chifukwa anthu achilendo andiukira,Ndipo anthu ankhanza akufunafuna moyo wanga.+ Iwo salemekeza Mulungu.*+ (Selah)   Taonani! Mulungu ndi amene amandithandiza.+Yehova amadalitsa anthu amene akundithandiza.   Iye adzabwezera adani anga+ zoipa zimene akuchitira anthu ena.Inu Mulungu wanga, awonongeni* chifukwa ndinu wokhulupirika.+   Ndidzapereka nsembe kwa inu+ mofunitsitsa. Inu Yehova, ndidzatamanda dzina lanu chifukwa ndi labwino.+   Inu mumandipulumutsa pa mavuto anga onse,+Ndipo ndidzayangʼana adani anga atagonja.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “ndiikireni kumbuyo pa mlandu wanga.”
Kapena kuti, “Iwo saika Mulungu patsogolo pawo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “akhalitseni chete.”