Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

FUNSO 8

Kodi Mulungu ndi Amene Amachititsa Kuti Anthu Azivutika?

“Nʼzosatheka kuti Mulungu woona achite zoipa, kapena kuti Wamphamvuyonse achite zinthu zolakwika.”

Yobu 34:10

“Munthu akakhala pa mayesero asamanene kuti: ‘Mulungu akundiyesa.’ Chifukwa Mulungu sangayesedwe ndi zinthu zoipa ndipo iye sayesa munthu ndi zinthu zoipa.”

Yakobo 1:​13

‘Muzimutulira nkhawa zanu zonse, chifukwa amakufunirani zabwino.’

1 Petulo 5:7

“Yehova sakuchedwa kukwaniritsa zimene analonjeza ngati mmene anthu ena amaonera kuti akuchedwa. Koma akukulezerani mtima chifukwa sakufuna kuti munthu aliyense adzawonongedwe, koma akufuna kuti anthu onse alape.”

2 Petulo 3:9