Salimo 38:1-22

  • Pemphero la munthu wovutika amene walapa

    • “Ndili ndi nkhawa komanso chisoni chachikulu” (6)

    • Yehova amayankha anthu amene amamuyembekezera (15)

    • “Tchimo langa linkandisowetsa mtendere” (18)

Nyimbo ya Davide ya chikumbutso. 38  Inu Yehova, musandidzudzule mutakwiya,Kapena kundilangiza mutapsa mtima.+   Chifukwa mivi yanu yandilasa kwambiri mpaka mkati,Ndipo dzanja lanu likundilemera.+   Thupi langa lonse likudwala* chifukwa cha mkwiyo wanu. Mʼmafupa anga mulibe mtendere chifukwa cha tchimo langa.+   Chifukwa zolakwa zanga zakwera kupitirira mutu wanga.+Sindingathe kuzisenza chifukwa zikulemera kwambiri ngati katundu wolemera.   Zilonda zanga zanyeka komanso zikununkhaChifukwa cha kupusa kwanga.   Ndili ndi nkhawa komanso chisoni chachikulu.Ndikuyendayenda ndili wachisoni tsiku lonse.   Ndikumva kuwotcha mʼthupi mwanga,*Thupi langa lonse likudwala.+   Thupi langa lonse lachita dzanzi ndipo ndilibiretu mphamvu.Ndikubuula mokweza* chifukwa cha kuvutika kwa mtima wanga.   Inu Yehova, mukudziwa zinthu zonse zimene ndikulakalaka,Nthawi zonse mumamva ndikamadandaula. 10  Mtima wanga ukugunda kwambiri komanso mphamvu zanga zatha,Ndipo maso anga achita mdima.+ 11  Anzanga komanso anthu amene ndimawakonda akundisala chifukwa cha mliri wanga,Ndipo anthu oyandikana nawo sakufuna kukhala nane pafupi. 12  Anthu amene akufunafuna moyo wanga anditchera misampha,Amene akufuna kundivulaza akukambirana zoti andiwononge,+Tsiku lonse iwo amapanga pulani yoti andinamize. 13  Koma ine ndakhala ngati munthu wogontha ndipo sindikumvetsera,+Ndakhala ngati munthu wosalankhula ndipo sindikutsegula pakamwa.+ 14  Ndakhala ngati munthu wosamva,Amene sangalankhule chilichonse podziteteza. 15  Chifukwa ine ndinayembekezera inu Yehova.+Ndipo inu Yehova Mulungu wanga, munandiyankha.+ 16  Ine ndinati: “Musalole kuti adani anga asangalale chifukwa cha mavuto angaKapena kuti adzikweze ngati phazi langa litaterereka.” 17  Chifukwa ndinali nditatsala pangʼono kugwa,Ndipo ndinkamva ululu nthawi zonse.+ 18  Ndinaulula cholakwa changa.+Tchimo langa linkandisowetsa mtendere.+ 19  Koma adani anga ndi amphamvu kwambiri,Ndipo odana nane popanda chifukwa anachuluka. 20  Iwo anandibwezera choipa mʼmalo mwa chabwino,Ndikafuna kuchita zabwino iwo ankandiletsa. 21  Inu Yehova, musandisiye. Inu Mulungu, musakhale kutali ndi ine.+ 22  Bwerani mwamsanga mudzandithandize,Inu Yehova, amene mumandipulumutsa.+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “Palibe malo abwino mʼthupi langa lonse.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Mʼchiuno mwanga mukuwotcha.”
Kapena kuti, “Ndikubangula.”