Salimo 107:1-43

 • Yamikani Mulungu chifukwa cha ntchito zake zodabwitsa

  • Anawayendetsa mʼnjira yabwino (7)

  • Anathetsa ludzu komanso njala ya anthu (9)

  • Anawatulutsa mumdima (14)

  • Ankalamula kuti achire (20)

  • Amateteza anthu osauka kuti asaponderezedwe (41)

107  Yamikani Yehova, chifukwa iye ndi wabwino.+Chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapobe mpaka kalekale.+   Anthu amene Yehova anawawombola anene zimenezi,Anthu amene anawawombola mʼmanja mwa mdani,*+   Anthu amene anawasonkhanitsa pamodzi kuchokera mʼmayiko osiyanasiyana,+Kuchokera kumʼmawa komanso kumadzulo,*Kuchokera kumpoto komanso kumʼmwera.+   Iwo ankayendayenda mʼchipululu mopanda kanthu.Sanapeze njira yopita kumzinda woti azikhalamo.   Anali ndi njala komanso ludzu.Anafooka kwambiri chifukwa chotopa.   Iwo anapitiriza kufuulira Yehova mʼmasautso awo,+Ndipo anawalanditsa ku mavuto awo.+   Anawayendetsa mʼnjira yabwino,+Kuti akafike kumzinda woti azikhalamo.+   Anthu ayamike Yehova+ chifukwa cha chikondi chake chokhulupirika,Ndiponso chifukwa cha ntchito zake zodabwitsa zimene wachitira ana a anthu.+   Chifukwa iye wathetsa ludzu la anthu aludzuNdipo anthu anjala wawadyetsa zinthu zabwino.+ 10  Ena ankakhala mumdima wandiweyani,Anali akaidi amene ankavutika atamangidwa maunyolo. 11  Chifukwa anapandukira mawu a Mulungu,Ananyoza malangizo a Wamʼmwambamwamba.+ 12  Choncho Mulungu anawagwetsera mavuto kuti akhale ndi mtima wodzichepetsa.+Iwo anapunthwa ndipo panalibe wowathandiza. 13  Iwo anaitana Yehova kuti awathandize mʼmasautso awo,Ndipo iye anawapulumutsa ku mavuto awo. 14  Iye anawatulutsa mumdima wandiweyani,Ndipo anadula maunyolo amene anamangidwa nawo.+ 15  Anthu ayamike Yehova chifukwa cha chikondi chake chokhulupirika,+Ndiponso chifukwa cha ntchito zake zodabwitsa zimene wachitira ana a anthu. 16  Chifukwa iye wathyola zitseko zakopa,*Komanso wadula mipiringidzo yachitsulo.+ 17  Anali opusa ndipo anakumana ndi mavuto+Chifukwa cha zolakwa zawo komanso machimo awo.+ 18  Analibe chilakolako* cha chakudya chilichonse,Iwo anayandikira khomo la imfa. 19  Iwo ankaitana Yehova kuti awathandize mʼmasautso awo.Ndipo iye ankawapulumutsa ku mavuto awo. 20  Iye ankalamula kuti achire ndipo ankachiradi+Komanso ankawapulumutsa kuti asafe. 21  Anthu ayamike Yehova chifukwa cha chikondi chake chokhulupirika,Ndiponso chifukwa cha ntchito zake zodabwitsa zimene wachitira ana a anthu. 22  Iwo apereke nsembe zoyamikira,+Komanso alengeze ntchito zake pofuula mosangalala. 23  Anthu amene amayenda panyanja mʼsitima,Amene amachita malonda pamadzi ambiri,+ 24  Iwo aona ntchito za Yehova,Ndiponso ntchito zake zodabwitsa mʼmadzi akuya.+ 25  Aona mmene mawu ake amayambitsira mphepo yamkuntho,+Nʼkuchititsa mafunde panyanja. 26  Mafundewo amakweza anthuwo mʼmwambaKenako amawatsitsa pansi pakati pa nyanja. Kulimba mtima kwawo kumatha chifukwa cha tsoka limene akuliyembekezera. 27  Amayenda peyupeyu ndipo amadzandira ngati munthu woledzera,Ndipo luso lawo lonse limakhala lopanda ntchito.+ 28  Kenako amafuulira Yehova mʼmasautso awo,+Ndipo iye amawapulumutsa mʼmavuto awo. 29  Iye amachititsa kuti mphepo yamkuntho ikhale bata,Mafunde apanyanja amadekha.+ 30  Iwo amasangalala mafundewo akatha,Ndipo Mulungu amawatsogolera kudoko limene iwo akufuna. 31  Anthu ayamike Yehova chifukwa cha chikondi chake chokhulupirika,Ndiponso chifukwa cha ntchito zake zodabwitsa zimene wachitira ana a anthu.+ 32  Amukweze mumpingo wa anthu,+Ndipo amutamande pamsonkhano* wa anthu achikulire. 33  Amasandutsa mitsinje kukhala chipululu,Ndiponso akasupe a madzi kukhala malo ouma.+ 34  Nthaka yobala zipatso amaisandutsa dziko lopanda chonde,+Chifukwa cha kuipa kwa anthu okhala mmenemo. 35  Chipululu amachisandutsa dambo la madzi,Ndipo dziko louma amalisandutsa dera la akasupe amadzi.+ 36  Amachititsa kuti anthu anjala azikhala kumeneko,+Kuti amangeko mzinda woti azikhalamo.+ 37  Anthuwo amafesa mbewu nʼkulima minda ya mpesa,+Kuti akhale ndi zokolola.+ 38  Mulungu amawadalitsa ndipo amachuluka kwambiri.Iye salola kuti ngʼombe zawo zichepe.+ 39  Koma iwo anakhala ochepa ndipo anachititsidwa manyaziChifukwa choponderezedwa, masoka komanso chisoni. 40  Mulungu amachititsa manyazi anthu olemekezekaNdipo amawachititsa kuti azingoyendayenda mʼchipululu mmene mulibe njira.+ 41  Koma amateteza* anthu osauka kuti asaponderezedwe+Ndipo amachulukitsa mabanja awo ngati gulu la nkhosa. 42  Olungama amaona zimenezi ndipo amasangalala.+Koma anthu onse osalungama amatseka pakamwa.+ 43  Aliyense wanzeru aona zinthu zimenezi+Ndipo aganizira mofatsa zimene Yehova wachita posonyeza chikondi chake chokhulupirika.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “anawawombola ku mphamvu za mdani.”
Kapena kuti, “Kuchokera kotulukira dzuwa komanso kolowera dzuwa.”
Kapena kuti, “zamkuwa.”
Kapena kuti, “Moyo wawo unkadana ndi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “pampando.”
Kapena kuti, “amakweza,” kutanthauza kuwaika pamalo amene aliyense sangafikepo.