Salimo 117:1, 2
-
Anthu a mitundu yonse akupemphedwa kuti atamande Yehova
-
Chikondi chokhulupirika cha Mulungu nʼchachikulu (2)
-
117 Tamandani Yehova, inu mitundu yonse ya anthu.+Mulemekezeni, inu anthu a mitundu yonse.*+
2 Chifukwa chikondi chokhulupirika chimene amatisonyeza ndi chachikulu.+Kukhulupirika+ kwa Yehova kudzakhalapo mpaka kalekale.+
Tamandani Ya!*+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “a mafuko onse.”
^ Kapena kuti, “Aleluya.” “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.