Salimo 121:1-8
Nyimbo Yokwerera Kumzinda.
121 Ndakweza maso anga kuyangʼana kumapiri.+
Kodi thandizo langa lichokera kuti?
2 Thandizo langa limachokera kwa Yehova,+Amene anapanga kumwamba ndi dziko lapansi.
3 Iye sadzalola kuti phazi lako literereke.*+
Amene akukuyangʼanira sadzawodzera.
4 Taonani! Amene akuyangʼanira Isiraeli,+Sadzawodzera kapena kugona.
5 Yehova akukuyangʼanira.
Yehova ndi mthunzi+ wako kudzanja lako lamanja.+
6 Masana dzuwa silidzakupweteka,+Kapenanso mwezi usiku.+
7 Yehova adzakuteteza ku zinthu zonse zimene zingakuvulaze.+
Iye adzateteza moyo wako.+
8 Yehova adzakuteteza pa zochita zako zonse,*Kuyambira panopa mpaka kalekale.
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “lipunthwe.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “pamene ukutuluka komanso pamene ukulowa.”