Salimo 51:1-19

  • Pemphero la munthu wolapa

    • Wochimwa kuchokera pamene mayi anatenga pakati (5)

    • ‘Ndiyeretseni ku machimo anga’ (7)

    • “Lengani mtima wolungama mkati mwanga” (10)

    • Mulungu amasangalala ndi kudzimvera chisoni mumtima (17)

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ya Davide, pa nthawi imene mneneri Natani anapita kwa iye, Davideyo atagona ndi Bati-seba.+ 51  Ndikomereni mtima inu Mulungu, mogwirizana ndi chikondi chanu chokhulupirika.+ Fufutani zolakwa zanga mogwirizana ndi chifundo chanu chachikulu.+  2  Mundisambitse bwinobwino nʼkuchotsa cholakwa changa,+Ndiyeretseni ku tchimo langa.+  3  Chifukwa zolakwa zanga ndikuzidziwa bwino,Ndipo tchimo langa lili pamaso panga* nthawi zonse.+  4  Inuyo ndi amene ndakuchimwirani kwambiri kuposa aliyense.*+Ndachita chinthu chimene mumachiona kuti ndi choipa.+ Choncho mukamalankhula, mumalankhula zachilungamo,Ndipo mukamaweruza, mumaweruza mwachilungamo.+  5  Taonani! Ndinabadwa ndili wochimwa,Ndipo ndine wochimwa kuchokera pamene mayi anga anatenga pakati panga.+  6  Taonani! Mumasangalala ndi choonadi chochokera pansi pa mtima.+Ndiphunzitseni* kuti ndikhale ndi mtima wanzeru.  7  Ndiyeretseni ndi hisope* ku machimo anga kuti ndikhale woyera.+Ndisambitseni kuti ndiyere kwambiri kuposa matalala.+  8  Ndichititseni kumva kufuula kokondwera ndi kosangalala,Kuti ndisangalale ngakhale kuti mwathyola mafupa anga.+  9  Ndikhululukireni* machimo anga,+Ndipo fufutani* zolakwa zanga zonse.+ 10  Inu Mulungu, lengani mtima wolungama mkati mwanga,+Ndipo sinthani mmene ndimaganizira+ kuti ndikhale wokhulupirika. 11  Musandichotse pamaso panu nʼkunditaya.Ndipo musandichotsere mzimu wanu woyera. 12  Bwezeretsani mwa ine chisangalalo chimene chimabwera chifukwa cha chipulumutso chanu.+Ndipatseni mtima wofunitsitsa kukumverani.* 13  Anthu olakwa ndidzawaphunzitsa njira zanu,+Kuti ochimwawo abwerere kwa inu. 14  Inu Mulungu, ndipulumutseni ku mlandu wa magazi,+ inu Mulungu wa chipulumutso changa,+Kuti lilime langa lilengeze mosangalala kuti ndinu wolungama.+ 15  Inu Yehova, tsegulani milomo yangayi,Kuti pakamwa panga patamande inu.+ 16  Chifukwa nsembe simukuifuna, mukanakhala kuti mukuifuna ndikanaipereka kwa inu.+Inu simusangalala ndi nsembe yopsereza yathunthu.+ 17  Nsembe zimene Mulungu amasangalala nazo ndi kudzimvera chisoni mumtima.Inu Mulungu, simudzakana* mtima wosweka ndi wophwanyika.+ 18  Chitirani Ziyoni zabwino mwa kukoma mtima kwanu.Ndipo mangani mpanda wa Yerusalemu. 19  Mukatero mudzasangalala ndi nsembe zachilungamo,Mudzakondwera ndi nsembe zopsereza komanso nsembe zathunthu.Pamenepo ngʼombe zamphongo zidzaperekedwa paguwa lanu la nsembe.+

Mawu a M'munsi

^ Kapena kuti, “mʼmaganizo mwanga.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Inu nokha.”
^ Kapena kuti, “Phunzitsani umunthu wanga wamkati.”
^ Kapena kuti, “Bisani nkhope yanu kuti isaone.”
^ Kapena kuti, “fafanizani.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndichirikizeni ndi mzimu wofunitsitsa.”
^ Kapena kuti, “simudzanyoza.”