Salimo 113:1-9
113 Tamandani Ya!*
Inu atumiki a Yehova, mutamandeni,Tamandani dzina la Yehova.
2 Dzina la Yehova litamandikeKuyambira panopa mpaka kalekale.+
3 Kuyambira kotulukira dzuwa mpaka kumene limalowera,Dzina la Yehova litamandidwe.+
4 Yehova ali pamwamba pa mitundu yonse ya anthu.+Ulemerero wake uli pamwamba pa kumwamba.+
5 Ndi ndani angafanane ndi Yehova Mulungu wathu,+Amene amakhala* pamwamba?
6 Iye amatsika mʼmunsi kuti aone kumwamba ndi dziko lapansi.+
7 Amadzutsa munthu wonyozeka kumuchotsa mʼfumbi.
Amanyamula munthu wosauka kumuchotsa pamulu wa phulusa*+
8 Kuti amukhazike pamodzi ndi anthu olemekezeka,Pamodzi ndi anthu olemekezeka pakati pa anthu a Mulungu.
9 Amachititsa mkazi wosabereka kukhala ndi anaKukhala mayi wosangalala wa ana.*+
Tamandani Ya!*

