Salimo 49:1-20

  • Kudalira chuma nʼkupusa

    • Palibe munthu amene angawombole mnzake (7, 8)

    • Mulungu amawombola munthu ku Manda (15)

    • Chuma sichingapulumutse munthu ku imfa (16, 17)

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ndi Salimo la ana a Kora.+ 49  Mvetserani izi, anthu nonsenu. Tcherani khutu anthu nonse okhala mʼdzikoli,*   Onyozeka ndi olemekezeka omwe,Olemera komanso osauka.   Pakamwa panga padzalankhula zinthu zanzeru,Ndipo zimene ndikuganizira mozama mumtima mwanga+ zidzasonyeza kuti ndine wozindikira.   Ndidzatchera khutu kuti ndimvetsere mwambi.Ndidzamasulira mawu anga ophiphiritsa poimba zeze.   Sindidzachita mantha pa nthawi yamavuto,+Pamene anthu oipa andizungulira kuti andivulaze.   Anthu amene akukhulupirira chuma chawo,+Amene amadzitamandira chifukwa cha kuchuluka kwa chuma chawo,+   Palibe ngakhale mmodzi wa iwo amene angathe kuwombola mʼbale wake,Kapena kumuperekera dipo kwa Mulungu,+   (Ndipo malipiro owombolera moyo* wawo ndi amtengo wapatali,Moti sangakwanitse kuwapereka),   Kuti akhale ndi moyo mpaka kalekale osaona dzenje la manda.+ 10  Aliyense amaona kuti ngakhale anthu anzeru amafa,Munthu wopusa komanso munthu wopanda nzeru, onse amawonongeka,+Ndipo chuma chawo amasiyira anthu ena.+ 11  Zimene mtima wawo umalakalaka nʼzakuti nyumba zawo zikhale mpaka kalekale,Matenti awo akhale ku mibadwomibadwo. Ndipo malo awo amawapatsa mayina awo. 12  Koma munthu, ngakhale kuti ndi wolemekezeka, sadzapitiriza kukhala ndi moyo mpaka kalekale.+Iye amangofanana ndi nyama zimene zimafa.+ 13  Izi ndi zimene zimachitikira anthu opusa,+Komanso anthu amene amawatsatira, amene amasangalala ndi mawu awo opanda pake. (Selah) 14  Iwo adzafa ngati nkhosa zimene zikupita kokaphedwa. Imfa idzakhala mʼbusa wawo.Mʼmawa anthu owongoka mtima adzawalamulira.+ Matupi awo adzawonongeka.+Kwawo kudzakhala ku Manda*+ osati mʼnyumba yachifumu.+ 15  Koma Mulungu adzandiwombola ku mphamvu ya* Manda,*+Chifukwa adzandigwira dzanja. (Selah) 16  Musachite mantha chifukwa chakuti munthu wina walemera,Kapena chifukwa chakuti katundu wamʼnyumba mwake wawonjezeka, 17  Chifukwa akadzamwalira sadzatenga china chilichonse.+Ulemerero wake sadzapita nawo limodzi.+ 18  Chifukwa pamene anali moyo ankatamanda moyo wake.+ (Anthu amakutamanda ukalemera.)+ 19  Koma pamapeto pake amafa ngati mmene makolo ake anachitira. Iwo sadzaonanso kuwala. 20  Munthu amene sazindikira zimenezi, ngakhale atakhala wolemekezeka,+Amangofanana ndi nyama zimene zimafa.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “a mʼnthawi ino.”
Kapena kuti, “Ndipo dipo lowombolera moyo.”
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼdzanja la.”
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.