Salimo 37:1-40

  • Anthu amene amadalira Yehova zinthu zimawayendera bwino

    • Usakhumudwe chifukwa cha anthu oipa (1)

    • “Uzisangalala chifukwa cha Yehova” (4)

    • “Lola kuti Yehova akutsogolere panjira yako” (5)

    • “Ofatsa adzalandira dziko lapansi” (11)

    • Olungama sadzasowa chakudya (25)

    • Olungama adzakhala padziko lapansi kwamuyaya (29)

Salimo la Davide. א [Aleph] 37  Usakhumudwe* chifukwa cha anthu oipaKapena kuchitira nsanje anthu ochita zoipa.+  2  Iwo adzafota mwamsanga ngati udzu+Ndipo adzanyala ngati msipu wobiriwira. ב [Beth]  3  Uzikhulupirira Yehova ndipo uzichita zabwino.+Ukhale padziko lapansi* ndipo uzichita zinthu mokhulupirika.+  4  Uzisangalala* chifukwa cha Yehova,Ndipo adzakupatsa zimene mtima wako umalakalaka. ג [Gimel]  5  Lola kuti Yehova akutsogolere panjira yako,*+Uzimudalira ndipo iye adzakuthandiza.+  6  Iye adzachititsa kuti kulungama kwako kuwale ngati mʼmawa,Ndipo chilungamo chako adzachichititsa kuti chiwale ngati dzuwa masana. ד [Daleth]  7  Khala chete pamaso pa Yehova+Ndipo umuyembekezere moleza mtima. Usakhumudwe ndi munthuAmene amakonza ziwembu nʼkuzikwaniritsa popanda vuto lililonse.+ ה [He]  8  Usapse mtima ndipo uzipewa kukwiya.+Usapse mtima nʼkuchita zoipa.*  9  Chifukwa anthu oipa adzaphedwa,+Koma amene akuyembekezera Yehova adzalandira dziko lapansi.+ ו [Waw] 10  Kwatsala kanthawi kochepa, ndipo oipa sadzakhalaponso.+Udzayangʼana pamene ankakhala,Ndipo sadzapezekapo.+ 11  Koma anthu ofatsa adzalandira dziko lapansi,+Ndipo adzasangalala ndi mtendere wochuluka.+ ז [Zayin] 12  Munthu woipa amakonzera chiwembu munthu wolungama,+Ndipo amamukukutira mano. 13  Koma Yehova adzamuseka,Chifukwa akudziwa kuti mapeto ake adzafika.+ ח [Heth] 14  Oipa asolola malupanga awo ndipo akunga mauta* awo,Kuti agwetse oponderezedwa ndi osauka,Kuti aphe anthu amene njira zawo ndi zolungama. 15  Koma lupanga lawo lidzalasa mtima wawo womwe,+Mauta awo adzathyoledwa. ט [Teth] 16  Zinthu zochepa zimene munthu wolungama ali nazo ndi zabwinoKusiyana ndi zinthu zochuluka za anthu ambiri oipa.+ 17  Chifukwa manja a anthu oipa adzathyoledwa,Koma Yehova adzathandiza anthu olungama. י [Yod] 18  Yehova amadziwa mavuto amene anthu osalakwa akukumana nawo,*Ndipo cholowa chawo chidzakhalapo mpaka kalekale.+ 19  Pa nthawi ya tsoka sadzachita manyazi,Ndipo pa nthawi ya njala adzakhala ndi chakudya chochuluka. כ [Kaph] 20  Koma oipa onse adzatheratu,+Adani a Yehova adzasowa mofulumira ngati malo okongola odyetsera ziweto amene msipu wake wobiriwira suchedwa kufota.Iwo adzatha mofulumira ngati utsi. ל [Lamed] 21  Munthu woipa amabwereka zinthu za ena koma osabweza,Koma wolungama amakhala wowolowa manja* ndipo amagawira ena zinthu zake.+ 22  Anthu amene Mulungu wawadalitsa adzalandira dziko lapansi,Koma amene wawatemberera adzaphedwa.+ מ [Mem] 23  Yehova akasangalala ndi njira za munthu+Amamusonyeza zoyenera kuchita pa moyo wake.+ 24  Ngakhale atapunthwa, sadzagweratu,+Chifukwa Yehova wamugwira dzanja kuti amuthandize.*+ נ [Nun] 25  Ndinali mwana ndipo tsopano ndakula,Koma sindinaonepo munthu aliyense wolungama atasiyidwa,+Kapena ana ake akupemphapempha chakudya.+ 26  Nthawi zonse amakongoza ena zinthu zake mokoma mtima,+Ndipo ana ake adzalandira madalitso. ס [Samekh] 27  Pewani kuchita zoipa ndipo muzichita zabwino,+Mukatero mudzakhala padziko lapansi mpaka kalekale. 28  Chifukwa Yehova amakonda chilungamo,Ndipo sadzasiya anthu ake okhulupirika.+ ע [Ayin] Adzawateteza nthawi zonse.+Koma mbadwa za anthu oipa zidzaphedwa.+ 29  Olungama adzalandira dziko lapansi,+Ndipo adzakhala mmenemo mpaka kalekale.+ פ [Pe] 30  Pakamwa pa munthu wolungama pamalankhula zinthu zanzeru,*Ndipo lilime lake limalankhula zinthu zachilungamo.+ 31  Chilamulo cha Mulungu wake chili mumtima mwake.+Iye adzachitsatira nthawi zonse.+ צ [Tsade] 32  Woipa amayangʼanitsitsa munthu wolungama,Ndipo amafuna kuti amuphe. 33  Koma Yehova sadzasiya wolungama mʼmanja mwa woipayo+Kapena kumupeza wolakwa akamaweruzidwa.+ ק [Qoph] 34  Yembekezera Yehova ndi kutsatira njira zake,Ndipo adzakukweza kuti ulandire dziko lapansi. Oipa akamadzaphedwa,+ iwe udzaona.+ ר [Resh] 35  Ine ndaona munthu wankhanza komanso woipaZinthu zikumuyendera bwino ngati mtengo wa masamba obiriwira bwino panthaka yake.+ 36  Koma anafa mwadzidzidzi ndipo sanapezekenso.+Ndinamufunafuna ndipo sindinamupeze.+ ש [Sin] 37  Onani munthu wosalakwa,*Ndipo yangʼanitsitsani munthu wolungama,+Chifukwa tsogolo la munthu ameneyo lidzakhala lamtendere.+ 38  Koma anthu onse ochimwa adzawonongedwa.Mʼtsogolo, anthu oipa adzaphedwa.+ ת [Taw] 39  Chipulumutso cha anthu olungama chimachokera kwa Yehova.+Iye ndi malo awo achitetezo champhamvu pa nthawi ya mavuto.+ 40  Yehova adzawathandiza nʼkuwapulumutsa.+ Adzawalanditsa kwa oipa nʼkuwapulumutsa,Chifukwa athawira kwa iye.+

Mawu a M'munsi

^ Kapena kuti, “Usakwiye.”
^ Kapena kuti, “mʼdzikoli.”
^ Kapena kuti, “Uzipeza chisangalalo chako chachikulu.”
^ Kapena kuti, “Pereka njira yako kwa Yehova.”
^ Mabaibulo ena amati, “chifukwa zimenezi zimatsogolera ku zoipa.”
^ Kapena kuti, “zingwe.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “amadziwa masiku a anthu osalakwa.”
^ Kapena kuti, “amakomera ena mtima.”
^ Kapena kuti, “akumuthandiza ndi Dzanja Lake.”
^ Kapena kuti, “pamalankhula zinthu zanzeru chapansipansi.”
^ Kapena kuti, “munthu wokhulupirika.”