Salimo 20:1-9

  • Kupulumutsidwa kwa mfumu yodzozedwa ya Mulungu

    • Ena amadalira magaleta ndi mahatchi, “koma ife timadalira dzina la Yehova” (7)

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ya Davide. 20  Yehova akuyankheni pa tsiku la mavuto. Dzina la Mulungu wa Yakobo likutetezeni.+   Akutumizireni thandizo kuchokera kumalo ake opatulika+Ndipo akuthandizeni ali ku Ziyoni.+   Akumbukire nsembe zanu zonse zimene munapereka monga mphatso.Alandire mosangalala* nsembe zanu zopsereza. (Selah)   Akupatseni zimene mtima wanu umalakalaka+Ndipo achititse kuti mapulani anu onse ayende bwino.*   Tidzafuula mosangalala chifukwa cha mmene mwatipulumutsira,+Tidzakweza mbendera zathu mʼdzina la Mulungu wathu.+ Yehova akwaniritse zopempha zanu zonse.   Tsopano ndadziwa kuti Yehova amapulumutsa wodzozedwa wake.+ Amamuyankha kuchokera kumwamba kwake koyera,Pomupulumutsa modabwitsa ndi dzanja lake lamanja.+   Ena amadalira magaleta ndipo ena amadalira mahatchi,+Koma ife timadalira dzina la Yehova Mulungu wathu.+   Anthu amenewo akomoka ndipo agwa,Koma ife tadzuka ndipo taimirira.+   Inu Yehova, pulumutsani mfumu!+ Tsiku limene tidzapemphe kuti atithandize, Mulungu adzatiyankha.+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “Aone ngati mafuta.”
Kapena kuti, “zolinga zanu zonse ziyende bwino.”