Salimo 149:1-9

  • Nyimbo yotamanda Mulungu chifukwa chopambana

    • Mulungu amasangalala ndi anthu ake (4)

    • Ulemerero ndi wa anthu onse okhulupirika a Mulungu (9)

149  Tamandani Ya!* Imbirani Yehova nyimbo yatsopano,+Mutamandeni mumpingo wa anthu ake okhulupirika.+  2  Isiraeli asangalale ndi Mlengi wake Wamkulu.+Ana a Ziyoni akondwere ndi Mfumu yawo.  3  Atamande dzina lake akuvina+Komanso kumuimbira nyimbo zomutamanda pogwiritsa ntchito maseche ndi zeze.+  4  Chifukwa Yehova amasangalala ndi anthu ake.+ Iye amakongoletsa anthu ofatsa ndi chipulumutso.+  5  Anthu okhulupirika asangalale chifukwa Mulungu amawalemekeza.Iwo aimbe mosangalala ali pamabedi awo.+  6  Pakamwa pawo patuluke nyimbo zotamanda Mulungu,Ndipo lupanga lakuthwa konsekonse likhale mʼmanja mwawo,  7  Kuti abwezere anthu a mitundu ina,Komanso kupereka chilango kwa mitundu ya anthu,  8  Ndiponso kuti amange mafumu awo maunyolo,Komanso kumanga anthu awo olemekezeka mʼmatangadza achitsulo.  9  Kuti awalange mogwirizana ndi chigamulo chimene chinalembedwa.+ Ulemerero umenewu ndi wa anthu onse okhulupirika a Mulungu. Tamandani Ya!*

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Aleluya.” “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.
Kapena kuti, “Aleluya.” “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.