Salimo 80:1-19
Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimboyi iimbidwe motsatira kaimbidwe ka “Nyimbo ya Maluwa.” Chikumbutso. Nyimbo ndi Salimo la Asafu.+
80 Inu Mʼbusa wa Isiraeli, mvetserani,Inu amene mukutsogolera Yosefe ngati gulu la nkhosa.+
Inu amene mwakhala pampando wachifumu pamwamba* pa akerubi,+Onetsani kuwala kwanu.*
2 Sonyezani mphamvu zanu+Pa Efuraimu, Benjamini ndi Manase.Bwerani mudzatipulumutse.+
3 Inu Mulungu, tibwezeretseni mwakale.+Walitsani nkhope yanu pa ife kuti tipulumutsidwe.+
4 Inu Yehova Mulungu wa magulu ankhondo akumwamba, kodi mudzakwiyira* anthu anu nʼkukana kumvetsera mapemphero awo mpaka liti?+
5 Mwawapatsa misozi kuti ikhale chakudya chawo,Ndipo mukuwamwetsa misozi yochuluka kwambiri.
6 Mwachititsa kuti anthu oyandikana nafe azikanganirana ifeyo.Adani athu akupitirizabe kutinyoza mmene akufunira.+
7 Inu Mulungu wa magulu ankhondo akumwamba, tibwezeretseni mwakale.Walitsani nkhope yanu pa ife kuti tipulumutsidwe.+
8 Munachititsa kuti mtengo wa mpesa+ uchoke mu Iguputo.
Munathamangitsa mitundu ya anthu kuti mudzalemo mtengowo.+
9 Munalambula malo odzalapo mtengo wa mpesawo,Ndipo unazika mizu nʼkudzaza dziko.+
10 Mapiri anaphimbika ndi mthunzi wake,Ndipo mitengo yamkungudza ya Mulungu inaphimbika ndi nthambi zake.
11 Nthambi zake zinakafika mpaka kunyanja,Ndipo mphukira zake zinafika ku Mtsinje.*+
12 Nʼchifukwa chiyani mwagwetsa mpanda wamiyala wa munda wampesawo,+Kuti anthu onse odutsa mumsewu azithyola zipatso zake?+
13 Nguluwe zamʼnkhalango zikuwononga mtengowo,Ndipo nyama zakutchire zikuudya.+
14 Inu Mulungu wa magulu ankhondo akumwamba, chonde bwererani.
Yangʼanani pansi pano muli kumwambako kuti muone,
Ndipo samalirani mtengo wa mpesa uwu,+
15 Mtengo umene dzanja lanu lamanja ladzala.+Ndipo muone mwana wanu amene munamupatsa* mphamvu kuti inu mulemekezeke.+
16 Wawotchedwa ndi moto+ nʼkudulidwa.
Anthu amawonongeka ndi kudzudzula kwanu.*
17 Dzanja lanu lithandize munthu amene ali kudzanja lanu lamanja,Lithandize mwana wa munthu amene mwamupatsa mphamvu kuti mulemekezeke.+
18 Mukatero ife sitidzakusiyani.
Tithandizeni kuti tikhalebe ndi moyo kuti titamande dzina lanu.
19 Inu Yehova Mulungu wa magulu ankhondo akumwamba, tibwezeretseni mwakale.Walitsani nkhope yanu pa ife kuti tipulumutsidwe.+
Mawu a M'munsi
^ Mabaibulo ena amati, “pakati.”
^ Kapena kuti, “Onetsani kunyezimira kwanu.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mudzalusira.”
^ Umenewu ndi mtsinje wa Firate.
^ Kapena kuti, “nthambi imene munaipatsa.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “kudzudzula kwa nkhope yanu.”