Pitani ku nkhani yake

Misonkhano ya Mpingo ya Mboni za Yehova

Dziwani zambiri zokhudza misonkhano yathu, ndiponso malo amene timachitira misonkhanoyi m’dera lanu.

Chidziwitso chokhudza matenda a Kolonavairasi (COVID-19): M'madera ambiri tasiya kaye kusonkhana m'Nyumba za Ufumu kapena kusonkhana anthu ambiri pamalo amodzi. Ngati mukufuna kudziwa zambiri, funsani wa Mboni za Yehova aliyense. Ponena za nkhani yapadera yamutu wakuti, “Kodi Ndi Mtsogoleri Uti Amene Tingamukhulupirire?,” tiika vidiyo ya nkhaniyi pawebusaiti yathu. Mungapange dawunilodi kapena kuonera vidiyoyi ngati simudzakwanitsa kukasonkhana nawo.

Fufuzani Malo Apafupi

Kodi Pamisonkhano Yathu Pamachitika Zotani?

Mboni za Yehova zimachita misonkhano kawiri pa mlungu yomwe cholinga chake n’kulambira Yehova. (Aheberi 10:24, 25) Aliyense amalandiridwa pamisonkhano imeneyi ndipo timaphunzira Baibulo, n’kukambirana mmene tingagwiritsire ntchito mfundo za m’Baibulozo pa moyo wathu.

Mbali yaikulu pamisonkhano imeneyi imachitika mokambirana, ngati mmene zimakhalira m’kalasi. Misonkhanoyi imayamba ndiponso kutha ndi nyimbo komanso pemphero.

Si zikudalira kuti mukhale wa Mboni za Yehova kuti mubwere kumisonkhano yathu. Aliyense ndi wolandiridwa. Malo okhala ndi aulere ndipo sitiyendetsa mbale ya zopereka.