Magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!
Magazini athu ofotokoza zokhudza Baibulo akupezeka m’zilankhulo zambiri, kuphatikizapo zinenero zamanja. Nsanja ya Olonda imafotokoza kwambiri za uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu komanso kutithandiza kuti tizikhulupirira Yesu Khristu. Galamukani! Imatithandiza kupirira mavuto amene timakumana nawo masiku ano komanso kutithandiza kuti tizidalira lonjezo la Mlengi wathu la kuti tidzakhala m’dziko latsopano la mtendere komanso chitetezo.

