Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

GALAMUKANI! Na. 1 2023 | Kodi Dzikoli Lidzakhalanso Bwino?—Pali Chiyembekezo

Simukufunika kukhala katswiri wa sayansi kuti muzindikire kuti dzikoli lawonongeka kwambiri. Madzi abwino, nyanja zikuluzikulu, nkhalango ngakhalenso mpweya zawonongekeratu. Kodi dzikoli lidzakhalanso bwino? Onani zifukwa zimene zingakuthandizeni kukhala ndi chiyembekezo.

 

Madzi Abwino

Kodi pali njira zachilengedwe zotani zomwe zimathandiza kuti madzi asathe padzikoli?

Nyanja Zikuluzikulu

Kodi nyanja zimene zawonongedwazi zingakonzedwenso?

Nkhalango

Kodi akatswiri azachilengedwe azindikira kuti chimachitika n’chiyani ndi nkhalango zimene zinawonongedwa?

Mpweya

Dzikoli linapangidwa m’njira yoti lizitha kupereka mpweya wabwino kwa chamoyo chilichonse. Kodi Mulungu anakhazikitsa njira zachilengedwe ziti zimene zimayeretsa mpweyawu ngati waipitsidwa?

Mulungu Akulonjeza Kuti Dzikoli Lidzakhalanso Bwino

Kodi tili ndi umboni wotani wotitsimikizira kuti dzikoli lidzakhalanso bwino ndipo lidzakhalapo mpaka kalekale?

Zimene Zili M’magaziniyi

Werengani nkhani zimene zili m’magaziniyi kuti mudziwe zimene zikuchitikira dzikoli komanso chifukwa chake pali chiyembekezo kuti lidzakhalanso bwino.