Pitani ku nkhani yake

‘Kondwerani Nthawi Zonse’

Msonkhano wa Mboni za Yehova wa 2020

Tikukulimbikitsani kuti mudzaonere msonkhano wa Mboni za Yehova wachaka chino. Msonkhanowu ndi wa masiku atatu. Chifukwa cha mliri wa kolonavairasi (COVID-19), msonkhano wachaka chino udzaonetsedwa kudzera pa intaneti pa jw.org. Zigawo zosiyanasiyana za msonkhanowu zizidzaikidwa pang’onopang’ono m’miyezi ya July ndi August.

ZINA ZOMWE ZIDZAKHALE PAMSONKHANOWU

  • Lachisanu: Dzaoneni zimene amuna okwatira, akazi okwatiwa, makolo komanso ana angachite kuti azikhala mosangalala m’banja mwawo. Mudzaphunziranso mmene chilengedwe chimasonyezera kuti Mulungu amafuna kuti tizisangalala.

  • Loweruka: N’chifukwa chiyani a Mboni za Yehova padziko lonse lapansi amauza ena uthenga wabwino wochokera m’Baibulo? Pamsonkhanowu padzakambidwa nkhani zosiyanasiyana, padzakhala mavidiyo komanso kufunsa ena mafunso ndipo zimenezi zidzakuthandizani kuphunzira zimene Malemba amanena pankhani yolalikira komanso kuphunzitsa.

  • Lamlungu: M’Baibulo muli lonjezo lakuti madalitso a Mulungu “ndi amene amalemeretsa, ndipo sawonjezerapo ululu.” (Miyambo 10:22) Mudzamvetsere nkhani ya m’Baibulo yakuti, “Kodi Mungatani Kuti Mukhale ndi Chuma Chomwe Sichiwonjezerapo Ululu?” ndipo mudzaone chifukwa chake muyenera kukhulupirira lonjezoli.

  • Vidiyo: Kodi kulimba mtima ndiponso khama limene munthu wina wotchulidwa m’Baibulo dzina lake Nehemiya anasonyeza zingakuthandizeni bwanji? Loweruka ndi Lamlungu, mudzaonera vidiyo yokhala ndi mbali ziwiri yamutu wakuti, “Chimwemwe Chimene Yehova Amapereka Ndicho Malo Anu Achitetezo.”Nehemiya 8:10.

SIMUDZALIPIRA NDALAMA

SIMUDZAFUNIKA KUPANGA LOGIN KAPENA KULEMBETSA

Onani pulogalamu ya msonkhano wonse komanso onerani vidiyo yofotokoza misonkhano yathu ikuluikulu.

Onerani Msonkhanowu