Pitani ku nkhani yake


KUPHUNZIRA BAIBULO MOTHANDIZIDWA NDI MUNTHU WINA

Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale

Muziphunzira Baibulo mokambirana komanso mwaulere. Panthawi yomwe mukuphunzira, mudzapeza mayankho a mafunso ngati awa:

  • Kodi ndingatani kuti ndizikhala wosangalala?

  • Kodi kuvutika ndiponso zinthu zoipa zidzathadi?

  • Kodi ndingadzakumanenso ndi achibale komanso anzanga omwe anamwalira?

  • Kodi Mulungu amasamaladi za ine?

  • Kodi ndizipemphera bwanji kuti Mulungu azimva mapemphero anga?

Simudzalipira Chilichonse

Simudzalipira ndalama panthawi yonse yomwe mudzakhale mukuphunzira. Buku lophunzirira la Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale komanso Baibulo, zidzakhala zaulere.

Potengera Zomwe Mungakonde

Muzikumana ndi mphunzitsi wanu pamasom’pamaso kapena muziphunzira kudzera pafoni kapena pa intaneti, panthawi ndi malo omwe mungakonde.

Simukukakamizidwa

Mutha kusintha nthawi ndi malo ophunzirira. Ndinu omasuka kunena ngati simukufuna kupitiriza kuphunzira.

Kodi Kuphunzirako Kumachitika Bwanji?

Mphunzitsi wanu adzakuthandizani kudziwa zomwe Baibulo limaphunzitsa, pophunzira mutu uliwonse pawokhapawokha. Pogwiritsa ntchito buku la Mungakhale Ndi Moyo mpaka Kalekale, mudzaphunzira Baibulo pang’onopang’ono ndipo mudzamvetsa bwino uthenga wake komanso mmene ungakuthandizireni. Kuti mudziwe zambiri, onerani vidiyoyi kapena pezani mayankho a mafunso omwe anthu amafunsa kawirikawiri pa nkhani ya mmene phunziroli limachitikira.

Mukufuna kuona nkhani zomwe zili m’bukuli?

Onani maphunziro oyambirira a m’bukuli.

Mukufuna Muyeserere?

Dinani mawu ali m’munsiwa kuti muyambe kuphunzira Baibulo.