Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

GALAMUKANI! Na. 1 2022 | Kodi Mungatani Kuti Mupirire Mavuto a M’Dzikoli?

Pamene zinthu m’dzikoli zikuipiraipira, anthufe tikukumana ndi mavuto osiyanasiyana obwera chifukwa cha ngozi zam’chilengedwe komanso oyambitsidwa ndi anthu. Onani zimene mungachite kuti mupirire mavutowa komanso kuti mudziteteze ndi kuteteza okondedwa anu

 

Kodi Mungatani Kuti Mupirire Mavuto a M’Dzikoli?

Mukakumana ndi mavuto muzikhala ofunitsitsa kuti mudziteteze komanso muteteze banja lanu.

1 | Muziteteza Thanzi Lanu

Mukamateteza thanzi lanu sizingakuvuteni kupirira mavuto amene mukumana nawo.

2 | Muzisamala Ndalama

Mukamagwiritsa ntchito bwino ndalama, sizingadzakuvuteni mukadzakumana ndi mavuto.

3 | Muziteteza Ubwenzi Wanu ndi Anzanu

Onani mfundo zimene zingakuthandizeni kuti muteteze banja lanu, ubwenzi wanu ndi anzanu komanso ndi ana anu.

4 | Muziteteza Chiyembekezo Chanu

Baibulo limatithandiza kupirira mavuto amene timakumana nawo komanso limatipatsa chiyembekezo chodalirika cha zimene zichitike m’tsogolo.

Zimene Zili M’magaziniyi

Werengani nkhani zimene zili m’magaziniyi zomwe zingakuthandizeni inuyo komanso anthu a m’banja lanu kupirira mavuto amene akuchitika masiku ano.