Mukuitanidwa
Mwambo Wokumbukira Imfa ya Yesu
Lachinayi, 2 April 2026
Tikukuitanirani ku zochitika ziwiri izi, zomwe ndi zaulere
Nkhani Yapadera ya M’Baibulo
“Kodi Ndi Ndani Adzakonze Zinthu Padzikoli?”
Dziwani zinthu zosangalatsa zimene Mulungu adzachitire anthu amene adzakhale padzikoli m’tsogolo.
Mwambo Wokumbukira Imfa ya Yesu
Pamwambo wofunika kwambiriwu, a Mboni za Yehova amakumbukira imfa ya Yesu mogwirizana ndi mmene Yesuyo analamulira.—Luka 22:19.
Mafunso Ofunsidwa Kawirikawiri
Ndi ndani akuyenera kubwera?
Aliyense ndi wolandiridwa. Mungabwere limodzi ndi banja lanu.
Kodi mwambowu udzatenga nthawi yaitali bwanji?
Nkhani yapadera ya m’Baibulo idzakhala ya 30 minitsi. Kenako padzakhala nkhani ina yokambirana za m’Baibulo kwa ola limodzi ndipo aliyense akhoza kudzayankhapo.
Mwambo wa Chikumbutso udzakhala wa ola limodzi.
Kodi zidzachitikira kuti?
Kuti mudziwe malo, dinani pamene alemba kuti “Kuti Mudziwe za Chikumbutso” kapena “Kuti Mudziwe za Nkhani Yapadera” m’mwambamu.
Kodi mwambowu udzakhala wolipiritsa?
Ayi.
Kodi padzakhala kuyendetsa mbale ya zopereka?
Ayi. A Mboni za Yehova samayendetsa mbale ya zopereka pamisonkhano yawo.—Mateyu 10:8.
Kodi tidzavale zovala zapadera?
Ayi. Komabe, a Mboni za Yehova amayesetsa kuvala moyenera komanso mwaulemu.
Kodi pamwambowu padzachitika zotani?
Mwambowu udzayamba komanso kutha ndi nyimbo komanso pemphero lomwe lidzaperekedwe ndi mtumiki wa Mboni za Yehova. Padzakhala nkhani yomwe idzafotokoze kufunika kwa imfa ya Yesu komanso mmene zomwe Mulungu ndi Khristu anatichitira zingatithandizire.
Kuti mudziwe zambiri, werengani nkhani yakuti “N’chifukwa Chiyani a Mboni za Yehova Mumachita Mwambo wa Mgonero wa Ambuye Mosiyana ndi Zipembedzo Zina?”
Kodi Chikumbutso chotsatira chidzachitika liti?
2026: Lachinayi, 2 April
2027: Lolemba, 22 March
2028: Lamlungu, 9 April
Kuti mudziwe zambiri, onerani mavidiyo otsatirawa.
Muvidiyoyi, muona mmene mwambowu umachitikira komanso muona mmene moyo udzakhalire m’tsogolo chifukwa cha imfa ya Yesu.
N’chifukwa Chiyani Yesu Anafa?
Mwina munamvapo kuti Yesu anafa chifukwa cha machimo athu. Koma kodi zingathekedi kuti imfa ya munthu mmodzi ithandize anthu mamiliyoni?
Kodi pa Nyumba ya Ufumu Pamachitika Zotani?
Muvidiyoyi muona zimene zimachitika m’Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova.
Pangani dawunilodi kapepala mufomati iliyonse.

