Pitani ku nkhani yake

Zokuthandizani Pophunzira Baibulo

Zinthuzi zingakuthandizeni kuti mupitirizebe kuphunzira Baibulo m’njira imene ingakupindulitseni komanso kukusangalatsani.

Werengani Baibulo pa Intaneti

Onani zimene zili mu Baibulo la Dziko Latsopano lomwe ndi lolondola komanso losavuta kuwerenga.

Mavidiyo Othandiza Pophunzira Baibulo

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Mabuku a M’Baibulo

Nkhani za m’mabuku a m’Baibulo komanso mmene zinthu zinalili pamene bukulo linkalembedwa.

Mavidiyo Othandiza Kumvetsa Mfundo Zofunika za M’Baibulo

Mavidiyo okhala ndi mayankho a mafunso ofunika kwambiri a m’Baibulo.

Malifalensi Komanso Zinthu Zothandiza Pophunzira Baibulo

Insayikulopediya ya Baibulo

Buku lakuti Insight on the Scriptures limafotokoza mawu masauzande ambiri. Mawuwo ndi okhudza zinthu monga anthu, malo, zomera, zinyama, zochitika zofunika komanso mawu ophiphiritsa a m’Baibulo. M’buku limene mungapange dawunilodi mulinso mapu, zithunzi, mlozera wa nkhani komanso wa malemba.

Mfundo Zachidule Zokhudza Baibulo

Kabuku kakuti Kodi Baibulo Lili ndi Uthenga Wotani? kamafotokoza momveka bwino mfundo zachidule za m’Baibulo ndipo kamathandiza anthu kudziwa mfundo yake yaikulu.

Kabuku Kosonyeza Mapu a Malo a M’Baibulo

M’kabuku kakuti ‘Onani Dziko Lokoma’ muli mapu ndi matchati osonyeza malo osiyansiyana a m’Baibulo, makamaka Dziko Lolonjezedwa pa nthawi zosiyanasiyana.

Vesi la M’Baibulo la Tsiku Lililonse

Kabuku ka Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku kofanana ndi kabuku ka mapemphero a m’mawa kapena ka kupembedza kwa m’mawa, kali ndi vesi la tsiku lililonse komanso ndemanga zachidule zofotokoza vesilo.

Njira Zothandiza Powerenga Baibulo

Ndandandayi ingakuthandizeni kwambiri kaya mukufuna kumangowerenga Baibulo tsiku lililonse, kukhala ndi cholinga chomaliza kuwerenga Baibulo chaka chimodzi kapena kutsatira ndondomeko yowerengera Baibulo ya anthu omwe angoyamba kumene.

Mmene Mungapezere Malemba M’Baibulo Lanu

Mndandanda wa mabuku 66 a m’Baibulo ndipo aikidwa mmene aliri m’Mabaibulo ambiri. Dzina la buku lalembedwa koyambirira kenako chaputala ndipo pomaliza vesi lake.

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Werengani kuti mudziwe mayankho a m’Baibulo a mafunso osiyanasiyana okhudza Mulungu, Yesu, banja, mavuto ndi zinthu zina zambiri.

Kufotokoza Mavesi a M’Baibulo

Dziwani tanthauzo lenileni la mavesi komanso mawu ena odziwika bwino a m’Baibulo.

Laibulale ya pa Intaneti (opens new window)

Fufuzani nkhani za m'Baibulo pa Intaneti m'mabuku a Mboni za Yehova.

Phunzirani Baibulo Ndi Munthu Wokuthandizani

Kodi Phunziro la Baibulo lomwe a Mboni za Yehova Amachititsa Limakhala Lotani?

Mukamaphunzira Baibulo kwaulere ndi a Mboni za Yehova, mungagwiritse ntchito Baibulo lililonse limene mukufuna. Mungapemphenso onse a m’banja lanu kapena mnzanu wina aliyense kuti akhale nanu pa phunzirolo.

Pemphani Kuti Tidzakuyendereni

Mutha kukhala ndi mwayi wokambirana nkhani inayake ya m’Baibulo kapena kudziwa zambiri zokhudza Mboni za Yehova.