Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Tingachite Kuti Nsembe ya Yesu Izitithandiza

Zimene Tingachite Kuti Nsembe ya Yesu Izitithandiza

 Chaka chilichonse, a Mboni za Yehova mamiliyoni ambiri padziko lonse ndi alendo awo amasonkhana pamodzi kuti achite mwambo wokumbukira imfa ya Yesu, monga mmene Yesu analamulira. (Luka 22:19) Mwambo umenewu umatithandiza kuti tiziyamikira zimene Yesu anatichitira popereka moyo wake monga nsembe m’malo mwa anthu onse. Umasonyezanso mmene nsembeyi ingatithandizire panopa komanso m’tsogolo.​—Yohane 3:16.

 Kaya mudzapezeka nawo pamwambo wa Chikumbutso wachaka chino kapena ayi, koma kodi nsembe ya Yesu ingakuthandizeni bwanji? Yesu anatiphunzitsa kuti tizichita zinthu ziwiri zofunika kwambiri izi:

  1.  1. Kuphunzira zokhudza Mulungu ndi Yesu. Popemphera kwa Atate wake wakumwamba, Yesu anati: “Pakuti moyo wosatha adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa za inu, Mulungu yekhayo amene ali woona, ndi za Yesu Khristu, amene inu munamutuma.”​—Yohane 17:3.

  2.  2. Kuchita zimene mumaphunzira. Yesu anatsindika kufunika kogwiritsa ntchito pa moyo wathu zimene amatiphunzitsa. Mwachitsanzo, m’mawu omaliza pa ulaliki wake wotchuka wapaphiri, anayamikira aliyense amene ‘amamva mawu ake, ndi kuwachita.’ (Luka 6:46-48) Pa nthawi inanso, iye ananena kuti: “Ngati zimenezi mukuzidziwa, ndinu odala mukamazichita.”​—Yohane 13:17.

 Kodi mungakonde kuphunzira zambiri zokhudza Mulungu ndi Yesu? Kodi mukufuna malangizo amene angakuthandizeni kuti muzichita zomwe mukuphunzira? Zinthu zotsatirazi zingakuthandizeni.

Phunziro la Baibulo

 Timaphunzira Baibulo ndi anthu kwaulere mochita kukambirana. Njira imeneyi yathandiza anthu ambiri kuti alidziwe bwino komanso kuti azigwiritsa ntchito mfundo zake pa moyo wawo.

  •   Pitani patsamba lakuti, Kuphunzira Baibulo Mothandizidwa Ndi Munthu Wina kuti mudziwe zambiri zokhudza phunziro la Baibulo limeneli.

  •   Onerani vidiyo yakuti, Sangalalani Pophunzira Baibulo kuti muone mmene phunziro la Baibulo ndi a Mboni za Yehova limachitikira.

Misonkhano ya a Mboni za Yehova

 A Mboni za Yehova amasonkhana kawiri pa mlungu kumalo awo olambirira omwe amatchedwa Nyumba ya Ufumu. Pamisonkhanoyi, timaphunzira Baibulo komanso kuona mmene tingagwiritsire ntchito mfundo zake pa moyo wathu.

 Aliyense ndi olandiridwa pamisonkhanoyi; ngakhale anthu amene si a Mboni. Mukhoza kusankha kukasonkhana pamasom’pamaso kapena kugwiritsa ntchito vidiyokomfelensi potengera mmene zinthu zilili m’dera lanu.

  •   Onerani vidiyo yakuti, Kodi pa Nyumba ya Ufumu Pamachitika Zotani? kuti muone mmene misonkhanoyi imachitikira.

Mavidiyo ndi nkhani za pa intaneti

 Pawebusaitiyi pali mavidiyo ndi nkhani zambiri zomwe zingakuthandizeni kuti muphunzire zambiri zokhudza zimene Yesu anaphunzitsa komanso kufunika kwa imfa yake.

 Mwachitsanzo, kodi zingatheke bwanji kuti imfa ya munthu mmodzi ithandize anthu mamiliyoni ambiri? Werengani nkhani yakuti, “Kodi Yesu Amatipulumutsa Bwanji?” komanso yakuti, “N’chifukwa Chiyani Yesu Anavutika Mpaka Kufa?” kapena onerani vidiyo yakuti, N’chifukwa Chiyani Yesu Anafa?