Nkhani Zina

Pamalowa mungapezepo nkhani zosiyanasiyana kuphatikizapo zomwe zili patsamba loyamba la jw.org. Werengani nkhani zimenezi komanso kuonera mavidiyo omwe alipo kuti mupeze nzeru zothandiza za m’Baibulo kuti mulimbitse chikhulupiriro chanu.

KHALANI MASO

Kunja Kukutentha Modetsa Nkhawa​—Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Kodi nthawi ina padzikoli sipadzapezekanso chamoyo chilichonse?

KHALANI MASO

Anthu Akuwononga Dziko Lapansi—Kodi Baibulo Limanena zotani?

Vesi lina la m’Baibulo limatchula zinthu zitatu zokhudza vuto la zachilengedwe lomwe lakhudza dziko lapansili.

KHALANI MASO

Kukwera Mitengo Kwa Zinthu Padziko Lonse—Kodi Baibulo Limanena Zotani?

N’chifukwa chiyani tikukumana ndi mavuto azachuma? Kodi Baibulo lingatithandize bwanji?

KHALANI MASO

Kuwombera M’masukulu—Kodi Baibulo Limanena Zotani?

N’chifukwa chiyani zinthu zoopsazi zimachitika? Kodi zinthu zachiwawa ngati zimenezi zingadzathedi?

KHALANI MASO

Nkhondo ya ku Ukraine Ikuwonjezera Vuto la Kuchepa Kwa Chakudya Padziko Lonse

Baibulo linaneneratu kale za mavuto a kusowa kwa chakudya. Komabe limatipatsa chiyembekezo komanso malangizo abwino omwe angatithandize polimbana ndi vutoli panopo.

KHALANI MASO

Anthu 6 Miliyoni Anamwalira ndi Matenda a COVID​—Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Baibulo linaneneratu kuti kudzakhala miliri yoopsa, limatitonthoza kuti tipirire mavuto amenewa, komanso limatiuza njira imene Mulungu adzagwiritse ntchito kuti adzathetse vutoli mpaka kalekale.

KHALANI MASO

Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani Yopembedza Zizindikiro

Kodi Mulungu zimam’khudza ngati timagwiritsa ntchito mafano komanso ziboliboli popemphera?

KHALANI MASO

Zomwe Zipembedzo Zikuchita pa Nkhondo ya ku Ukraine​—Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Kumbali zonse, atsogoleri amatchalitchi ali ndi maganizo osiyana kwambiri ndi zomwe Yesu anaphunzitsa otsatira ake kuti azichita komanso zoti asamachite.

KHALANI MASO

Anthu Ambirimbiri Athawa Nkhondo M’dziko la Ukraine

Baibulo limafotokoza zifukwa zenizeni zomwe zachititsa vutoli komanso mmene mavutowa adzathere mpaka kalekale.

Mfundo za M’Baibulo Zomwe Zingakuthandizeni Ngati Mwachotsedwa Ntchito

Phunzirani njira zokwanira 6 zomwe zingakuthandizeni.

Asilikari a Dziko la Russia Alowa M’dziko la Ukraine

Ngati ndi choncho, kodi Baibulo limafotokoza mmene zimenezi zithere?

Kodi Katangale Adzatha M’Boma?

Onani zifukwa zitatu zomwe zikutitsimikizira za boma linalake lapadera kuti silidzachita zachinyengo.

Kodi Moyo Udzabwereranso Mwakale?Mmene Baibulo Lingakuthandizireni M’nthawi ya Mliri.

Mfundo 6 za m’Baibulo zingatithandize kudziwa zoyenera kuchita komanso kupirira mavuto omwe akubwera m’tsogolomu.

Kodi Zipembedzo Ziyenera Kuchita Nawo Zandale?

Padziko lonse, anthu omwe amati ndi otsatira a Yesu Khristu amalowerera kwambiri munkhani zandale. Kodi ayeneradi kumachita zimenezi?

Kodi Mayiko Angathe Kuyendetsa Chuma Mokomera Aliyense?

Pali boma limene lingathe kulamulira dziko lapansi m’njira yabwino kwambiri, n’kuthetseratu umphawi ndi mavuto azachuma.

Kodi Baibulo Lingakuthandizeni Pakachitika Ngozi Zam’chilengedwe?

Malangizo a m’Baibulo angakuthandizeni pasanachitike ngozi zam’chilengedwe, pamene zikuchitika komanso pambuyo pake.

Kodi Uchigawenga Udzatha?

Mpaka nthawi imene zonse zochititsa mantha komanso zachiwawa zidzathe, zinthu ziwiri zimene Baibulo limatilimbikitsa kuchita zingathandize anthu omwe akhudzidwa ndi zauchigawenga.

Kodi Dzikoli Lidzatha? Kodi Baibulo Limanena Kuti Zinthu Zonse Zidzawonongedwa?

Ngakhale kuti Baibulo limanena kuti dzikoli lidzakhala mpaka kalekale, pali dziko limene lidzathe.

Dzitetezeni Kuti Musamapusitsidwe ndi Nkhani Zabodza

Nkhani zolakwika, malipoti abodza ndi nkhani zamphekesera zafala kwambiri ndipo zingakubweretsereni mavuto.

Zimene Mungachite Mukaferedwa

Muone zinthu zimene zingakuthandizeni kupirira.

Kodi Tingatani Kuti Tisamade Nkhawa Kwambiri?

Kodi ndi mavesi a m’Baibulo ati komanso zinthu ziti zimene zingakuthandizeni kuti musamade nkhawa kwambiri?

Tiziyembekezera Kuti Zinthu Zidzakhala Bwino M’tsogolo

N’chifukwa chiyani tinganene kuti malonjezo a m’Baibulo ndi osiyana ndi malonjezo komanso maganizo a anthu?

Kodi Chipembedzo Chasanduka Bizinezi Yotentha?

Nthawi zina anthu amene amabwera kutchalitchi ndi osauka, pomwe m’busa wa tchalitchicho ndi wolemera kwambiri.

Kodi Ndi Ndani Amene Adzapulumutse Dzikoli?

Akatswiri ena a chilengedwe amanena kuti zimene anthu akuchita panopa zikhoza kuwonongeratu mitundu ina ya zinyama ndi zitsamba.

Baibulo Lingathandize Amuna Amene Ali Ndi Nkhawa

Nkhawa ndi vuto lalikulu kwambiri popeza tili munthawi yapadera komanso yovuta, ndiye kodi Baibulo lingakuthandizeni?

Zimene Zingatithandize Ngati Tatopa ndi Mliri

Ngati sitichita zinthu zimene zingatithandize kuti tisatope ndi mliriwu, pang’ono ndi pang’ono tingayambe kugwa ulesi pa nkhani yotsatira malangizo otitetezera ku COVID-19.

Kodi Zinthu Zopanda Chilungamo Zidzatha Padzikoli?

Baibulo limasonyeza kuti chilungamo chenicheni chimachokera kwa Mulungu amene amaona kuti moyo wa munthu aliyense ndi wofunika.

Baibulo la Dziko Latsopano Lokonzedwanso Linatulutsidwa M’Chisipanishi

Kodi omasulira Baibulo anakwanitsa bwanji kumasulira Baibulo limene mawu amodzi amatanthauza zinthu zingapo m’madera ena apadziko lapansi?

Zimene Zingakuthandizeni Ngati Mwayamba Kudwala Mwadzidzidzi

Kodi ndi mfundo ziti za m’Baibulo zimene zingakuthandizeni ngati mwayamba kudwala mosayembekezereka?

Zimene Mungachite Ngati Mukupeza Ndalama Zochepa

Mavuto azachuma akabwera mwadzidzidzi zimadetsa nkhawa, koma mfundo za m’Baibulo zingakuthandizeni kuti muzitha kugwiritsa ntchito ndalama zochepa.

Mungatani Kuti Musayambe Kumwa Mowa Mopitirira Malire?

Mfundo 5 zimene zingakuthandizeni kuti musamamwe mowa mopitirira malire ngakhale pamene muli ndi nkhawa kwambiri.

Mfundo Zothandiza Anthu Omwe Achitiridwa Nkhanza Zosiyanasiyana

Dziwani kuti wolakwa si inuyo ndipo sikuti muli nokha.

Zimene Mungachite Ngati Muli Nokhanokha

Mukamamva kuti muli nokhanokha, mungayambe kuona kuti simungathe kupeza chiyembekezo, chimwemwe komanso kukhala wokhutira​—komatu si choncho.

Kodi Yohane M’batizi Anakhalapodi?

Katswiri wolemba mbiri yakale dzina lake Josephus anatsimikizira mfundo yakuti Yohane M’batizi anakhalapodi. Choncho ifenso tiyenera kukhulupirira mfundo imeneyi.

Zolemba Zakale Zimapereka Umboni Wosonyeza Malo Amene Aisiraeli Ankakhala

Mapale a ku Samariya amasonyeza kuti zomwe Baibulo limanena zokhudza mbiri yakale ndi zoona.

Kodi Zidindo Zakale Zinkagwira Ntchito Yanji?

N’chifukwa chiyani zidindo zakale zinali zofunika, nanga olamulira ankazigwiritsa ntchito bwanji?

Kodi Zimene Baibulo Limanena Zokhudza Ukapolo wa Ayuda ku Babulo N’zolondola?

Kodi zimene akatswiri ofufuza anapeza zikugwirizana bwanji ndi zimene Mulungu ananena zokhudza moyo wa Ayuda ali ku ukapolo ku Babulo?

Chipilala Chakale cha ku Iguputo Chili Ndi Umboni wa Nkhani ya M’Baibulo

Werengani nkhaniyi kuti muone mmene zolemba zakale za ku Iguputo zimasonyezera kuti anthu omwe analemba Baibulo anali oona mtima.

Mulungu Anapereka Mfundo Zokhudza Ukhondo Asayansi Asanazitulukire

Aisiraeli zinthu zinkawayendera bwino chifukwa chotsatira malangizo a Mulungu okhudza ukhondo.

Zimene Asayansi Afukula Zikutsimikizira Kuti Mfumu Davide Analikodi

Anthu ena amanena kuti Mfumu Davide kunalibe ndipo nkhani yake ndi yongopeka. Kodi asayansi apeza umboni wotani?

Dzina la Mulungu Limapezekanso mu Mpukutu Wakale

Onani umboni wosonyeza kuti dzina la Mulungu linkapezeka mu “Chipangano Chatsopano.”

Njira Zowerengera Baibulo

Ndandandayi ingakuthandizeni kwambiri kaya mukufuna kumangowerenga Baibulo tsiku lililonse, kukhala ndi cholinga chomaliza kuwerenga Baibulo chaka chimodzi kapena kutsatira ndondomeko yowerengera Baibulo ya anthu omwe angoyamba kumene.

Kodi Moyo Unayamba Bwanji?

Zoona zake n’zakuti pali anthu ambiri ophunzira kuphatikizapo asayansi ena omwe amakayikira zoti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina.

Mmene Mungapezere Malemba M’Baibulo Lanu

Mndandanda wa mabuku 66 a m’Baibulo ndipo aikidwa mmene aliri m’Mabaibulo ambiri. Dzina la buku lalembedwa koyambirira kenako chaputala ndipo pomaliza vesi lake.

Ankalemekeza Kwambiri Baibulo

William Tyndale komanso Michael Servetus ali m’gulu la anthu omwe ankatsutsidwa komanso kuopsezedwa kuti aphedwa. Iwo analolera kuika moyo wawo pangozi n’cholinga chofuna kuteteza choonadi cha m’Baibulo.

Ankalemekeza Kwambiri Baibulo—Kachigawo ka Vidiyo (William Tyndale)

Umboni wakuti ankakonda kwambiri Baibulo umaonekera mu ntchito imene anagwira imene imatithandizabe masiku ano.

Pepani, palibe mawu ofanana ndi omwe mwasankha