Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

mustafahacalaki/DigitalVision Vectors via Getty Images

KHALANI MASO

Kodi Nzeru Zopangidwa Ndi Anthu, N’zothandizadi Kapena Zingayambitse Mavuto?—Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Kodi Nzeru Zopangidwa Ndi Anthu, N’zothandizadi Kapena Zingayambitse Mavuto?—Kodi Baibulo Limanena Zotani?

 Posachedwapa, atsogoleri a mayiko, asayansi, akatswiri a luso la zipangizo zamakono alankhulapo pa nkhani yokhudza ubwino kapena kuipa kwa nzeru zopangidwa ndi anthu. a Ngakhale akuona kuti zinthuzi ndi zofunika, akuda nkhawa kuti zikhoza kuyambitsa mavuto ngati zitapanda kugwiritsidwa ntchito moyenerera.

  •   “Masiku ano, nzeru zopangidwa ndi anthu zikugwiritsidwa ntchito kwambiri poganiza kuti zingathe kusintha moyo wa anthu . . . Komabe pangapezeke mavuto ambiri omwe angabweretse chiopsezo pa nkhani yachitetezo, ufulu wachibadwidwe, kusunga chinsinsi komanso kuchititsa anthu kuti asiye kukhulupirira demokalase.”​—Kamala Harris, wachiwiri kwa pulezidenti wa dziko la United States, May 4, 2023.

  •   “Ngakhale kuti nzeru zopangidwa ndi anthu zikuthandiza kwambiri pa nkhani ya zachipatala, zikubweretsa mavuto ambiri azaumoyo,” linatero gulu la madokotala am’mayiko osiyanasiyana ndi akatswiri azaumoyo motsogoleredwa ndi Dr. Frederik Federspiel, munkhani ya pa May 9, 2023, m’kabuku kakuti, BMJ Global Health. b

  •   “Anthu ayamba kale kufalitsa nkhani zabodza pogwiritsa ntchito nzeru zopangidwa ndi anthu. Posachedwapa, nzeru zimenezi zingachititse kuti anthu ambiri achotsedwe ntchito. Anthu ogwira ntchito yokhudzana ndi luso la zipangizo zamakono akuda nkhawa kuti nzeruzi zingabweretse chiopsezo pa moyo wa anthu.”​—The New York Times, May 1, 2023.

 M’kupita kwa nthawi, anthu adzadziwa ngati nzeru zopangidwa ndi anthu zingakhaledi zothandiza kapena zobweretsa mavuto. Kodi Baibulo limanena zotani?

Nzeru za anthu zikuchititsa kuti anthu azidziona kuti ndi osatetezeka

 Baibulo limasonyeza chifukwa chake sitingadalire kuti zipangizo zamakono zimene anthu akupanga masiku ano zingachititse kuti zinthu ziziyenda bwino padzikoli.

  1.  1. Ngakhale anthu atakhala ndi zolinga zabwino, sangadziwiretu mavuto amene angadzachitike m’tsogolo chifukwa cha zinthu zimene akuchita panopa.

  2.  2. Munthu alibe mphamvu zoletsa anthu ena kugwiritsa ntchito molakwika zinthu zimene iyeyo wapanga.

    •   “Ntchito yonse [yomwe ndagwira] . . . ndidzasiyire munthu amene akubwera pambuyo panga. Ndipo kodi ndani angadziwe kuti kaya adzakhala wanzeru kapena wopusa? Koma adzatenga zinthu zanga zonse zimene ndinazipeza movutikira ndiponso zimene ndinazichita mwanzeru padziko lapansi pano. Zimenezinso n’zachabechabe.”​—Mlaliki 2:18, 19.

 Zimenezi zikusonyeza chifukwa chake timafunikira kutsogoleredwa ndi Mlengi wathu.

Kodi tiyenera kudalira ndani?

 Zimene Mlengi wathu anatilonjeza zikutitsimikizira kuti iye sadzalola kuti anthu kapena zinthu monga zipangizo zilizonse zamakono, ziwononge dzikoli kapenanso mtundu wonse wa anthu.

  •   “Dziko lapansi lidzakhalapobe mpaka kalekale.”​—Mlaliki 1:4.

  •   “Olungama adzalandira dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.”​—Salimo 37:29.

 Mlengi wathu amatipatsa malangizo kudzera m’Baibulo amene angatithandize kudzakhala ndi moyo wamtendere komanso wotetezeka. Kuti mudziwe zambiri zokhudza zimene Baibulo limanena pa nkhaniyi, werengani nkhani zakuti, “Kodi Malangizo Odalirika Okhudza Tsogolo Labwino Tingawapeze Kuti?” komanso “Tiziyembekezera Kuti Zinthu Zidzakhala Bwino M’tsogolo.”

a “Nzeru zopangidwa ndi anthu” (Artificial intelligence kapena kuti “AI”) zikutanthauza makompyuta kapena makina oyendetsedwa ndi makompyuta, manetiweki kapenanso luso la zipangizo zamakono zomwe zimakonzedwa m’njira yoti zizitha kuphunzira kapena kutengera mmene anthu amaganizira komanso kuchitira zinthu.

b Kuchokera munkhani yakuti, “Threats by Artificial Intelligence to Human Health and Human Existence,” yolembedwa ndi Frederik Federspiel, Ruth Mitchell, Asha Asokan, Carlos Umana, komanso David McCoy.