Pitani ku nkhani yake

Zokhudzana ndi Malamulo Komanso Ufulu Wachibadwidwe

 

Maofesi Oona Zamalamulo

Ma adiresi ndi manambala a foni a maofesi athu oona zamalamulo.

Articles

2018-08-09

RUSSIA

A Mboni Enanso ku Russia Anamangidwa Apolisi Atathyola Nyumba Zawo

Akuluakulu a boma la Russia akhala akuchitira a Mboni zinthu zankhanza, kuwamanga komanso kuwaika m’ndende chifukwa chochita zinthu zokhudzana ndi chikhulupiriro chawo.

2017-07-25

SOUTH KOREA

“Chigamulo cha Khoti Chabwino Kwambiri Chaka Chino”

Khoti la Apilo la Gwangju linagamula kuti anyamata atatu ndi osalakwa pa mlandu womwe ankaimbidwa chifukwa chokana usilikali. Aliyense akuyembekezera kuti khoti lapamwamba kwambiri lipereke chigamulo chake.

2016-12-22

TURKMENISTAN

Kodi a Bahram Hemdemov Amasulidwa Nawo Ulendo Ukubwerawu?

A Mboni za Yehova akuyembekezera kuti pa ulendo wotsatira wotulutsa anthu m’ndende, mtsogoleri wa dziko la Turkmenistan a Gurbanguly Berdimuhamedov adzatulutsanso a Hemdemov.

2018-01-17

UKRAINE

Khoti Lalikulu ku Ukraine Linalimbikitsa Ufulu Wosonkhana Mwamtendere

Panopo a Mboni za Yehova ku Ukraine akhoza kupanga lendi malo kuti achitiremo mapemphero popanda kukanizidwa.

2018-01-17

GEORGIA

Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe Lathandiza Kuti a Mboni za Yehova Akhale ndi Ufulu Wopembedza ku Georgia

Chigamulo chaposachedwapa cha Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe chikuteteza ufulu wa a Mboni wosonkhana pamodzi n’cholinga cholambira Mulungu komanso kuuza ena zimene amakhulupirira mwamtendere.

2018-06-15

RUSSIA

Wa Mboni Winanso ku Russia Akuimbidwa Mlandu Wochita Zinthu Zoopsa

A Arkadya Akopyan, ndi a Mboni za Yehova ndipo ali ndi zaka 70 komanso anapuma pa ntchito ya utelala. Bambowa ndi osalakwa, amamvera malamulo a boma ndipo cholinga chawo n’choti azipembedza Mulungu mwamtendere.

2018-08-09

RUSSIA

Khoti la ku Oryol Limvetsera Umboni Koyamba pa Mlandu wa a Dennis Christensen

A Dennis Christensen akhala akusungidwa m’ndende kuyambira mu May 2017. Iwo akhoza kupatsidwa chilango chokhala m’ndende kwa zaka 6 mpaka 10 chifukwa chongochita zinthu zogwirizana ndi zimene amakhulupirira.