Pitani ku nkhani yake

Kodi Ndalama Zoyendetsera Ntchito Yanu Zimachokera Kuti?

Kodi Ndalama Zoyendetsera Ntchito Yanu Zimachokera Kuti?

Ndalama zoyendetsera ntchito yathu kwenikweni zimachokera kwa ifeyo a Mboni za Yehova ndipo timapereka mwa kufuna kwathu. Sitiyendetsa mbale ya zopereka pa misonkhano yathu ndiponso sitipereka chakhumi. (Mateyu 10:7, 8) M’malomwake, pamisonkhano yathu pamaikidwa mabokosi a zopereka kuti amene angafune kupereka aponye mmenemo. Sitilengeza mayina a anthu amene apereka.

Ndalama zimene timapeza zimakwanira kuyendetsera ntchito yathu chifukwa tilibe abusa amene timawalipira. Chifukwa chinanso n’chakuti, sitilipidwa kuti tizikalalikira nyumba ndi nyumba, komanso malo athu olambirira samangidwa m’njira yoti athe ndalama zambiri.

Zopereka zimene zimatumizidwa kumaofesi a Mboni za Yehova zimagwiritsidwa ntchito kuthandiza anthu amene akhudzidwa ndi masoka a chilengedwe, kuthandizira a mishonale ndi atumiki amene amayendera mipingo yathu. Zimathandiziranso pa ntchito yamanga nyumba zolambiriramo m’mayiko osauka komanso kusindikiza ndi kutumiza mabaibulo ndi mabuku ena ofotokoza nkhani za m’Baibulo.

Munthu aliyense amasankha yekha ngati akufuna kupereka ndalama zothandizira pa ntchito yolalikira imene ikuchitika padziko lonse kapena zothandizira pa mpingopo. Munthu akhoza kusankhanso kupereka ndalama zothandizira pa ntchito zonsezi. Mwezi ndi mwezi, mpingo uliwonse umadziwitsa anthu a mu mpingomo mmene ndalama zagwirira ntchito.