Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Kodi a Mboni za Yehova Ali ndi Baibulo Lawolawo?

Kodi a Mboni za Yehova Ali ndi Baibulo Lawolawo?

A Mboni za Yehova akhala akugwiritsa ntchito Mabaibulo osiyanasiyana pophunzira Baibulo. Komabe timagwiritsa ntchito kwambiri Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika ngati lilipo m’chinenero chathu. Timalikonda Baibulo limeneli chifukwa chakuti limagwiritsa ntchito dzina la Mulungu, linamasuliridwa molondola komanso ndi losavuta kumva.

  • Kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu. Anthu ena omasulira Baibulo anatchula maina a anthu amene anathandiza pa ntchito yomasulira koma analephera kupereka ulemu kwa munthu amene analemba Baibulo. Mwachitsanzo, m’Baibulo lina analembamo mayina oposa 70 a anthu amene anathandizira nawo pa ntchito yomasulira Baibuloli. Koma n’zodabwitsa kuti m’Baibuloli sanatchulemo ngakhale kamodzi dzina la Mulungu lakuti Yehova, yemwe analemba Baibulo.

    Mosiyana ndi zimenezi, komiti ya anthu amene anamasulira Baibulo la Dziko Latsopano anabwezeretsa dzina la Mulungu m’malo ambirimbiri amene dzinali linkapezeka m’Baibulo loyambirira. Chochititsa chidwi n’chakuti anthu a m’komitiyi mayina awo sadziwika mpaka pano.

  • Kumasuliridwa molondola. Si Mabaibulo onse amene anamasulira molondola uthenga umene unali m’Baibulo loyambirira. Mwachitsanzo, m’Baibulo lina anamasulira mawu a palemba la Mateyu 7:13 motere: “Lowani pachipata chopapatiza. Pakuti chipata chopita ku gehena ndi chotakasuka ndipo msewu wopita kumeneko ndi wosavuta kuyenda.” Koma m’Baibulo loyambirira anagwiritsira ntchito mawu akuti “chiwonongeko,” osati “gehena.” Mwina amene anamasulira Baibuloli anaika mawu akuti “gehena” chifukwa ankakhulupirira kuti anthu oipa adzawotchedwa kwamuyaya kugehena. Koma Baibulo siliphunzitsa zimenezi. N’chifukwa chake palembali, Baibulo la Dziko Latsopano limanena molondola kuti: “Lowani pachipata chopapatiza. Pakuti msewu waukulu ndi wotakasuka ukupita kuchiwonongeko.”

  • Kumveka mosavuta. Baibulo lomasuliridwa molondola limafunikanso likhale losavuta kumva. Taonani chitsanzo ichi. Palemba la Aroma 12:11, mtumwi Paulo anagwiritsira ntchito mawu amene kungotengera mmene mawuwo alili amatanthauza “mpaka mzimu kuwira.” Popeza mawuwa ndi ovuta kumva m’chingerezi, Baibulo la Dziko Latsopano linatchula mawuwa m’njira yosavuta kumva. Baibuloli linanena kuti Akhristu ayenera ‘kuyaka ndi mzimu.’

Kuwonjezera pa kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu, kumasuliridwa molondola komanso kusavuta kumva, Baibulo la Dziko Latsopano lilinso ndi ubwino wina. Ubwino wake ndi wakuti Baibuloli limaperekedwa mopanda mtengo weniweni koma anthu amapereka ndalama mwakufuna kwawo. Izi zathandiza kuti anthu mamiliyoni ambiri amene mwina sakanakwanitsa kugula, aziwerenga Baibulo m’chinenero chawo.