Pitani ku nkhani yake

Kodi Mumagwira Nawo Ntchito Yothandiza Ena Pakagwa Tsoka?

Kodi Mumagwira Nawo Ntchito Yothandiza Ena Pakagwa Tsoka?

Inde, a Mboni za Yehova nthawi zambiri amathandiza ena pakagwa tsoka. Timathandiza anthu a Mboni anzathu komanso omwe si a Mboni. Timachita zimenezi potsatira malangizo a m’Baibulo opezeka pa Agalatiya 6:10 akuti: “Tiyeni tichitire onse zabwino, koma makamaka abale ndi alongo athu m’chikhulupiriro.” Pa nthawi yovutayi, timayesetsanso kuthandiza anthu amene akhudzidwa ndi tsokalo powatonthoza komanso kuwalimbikitsa ndi mfundo za m’Baibulo.—2 Akorinto 1:3, 4.

Dongosolo

Pakachitika tsoka, akulu a m’mipingo ya m’dera limene lakhudzidwalo amayesetsa kufufuza anthu onse amene amasonkhana m’mipingoyo kuti adziwe ngati ali bwino komanso kuti adziwe chithandizo chimene angafunikire. Kenako akuluwo amatumiza lipoti la zimene apezazo komanso la thandizo lamwansanga limene apereka kwa anthuwo ku ofesi ya Mboni za Yehova ya m’deralo ndipo ndondomeko yothandizira anthuwo imakonzedwa.

Ngati mipingo ya m’deralo singakwanitse kupereka chithandizo chonse chofunikira kwa anthu amene akhudzidwawo, Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova limakonza dongosolo lina lothandizira anthuwo. Zimenezi n’zofanana ndi zimene Akhristu oyambirira ankachita pothandiza anzawo pa nthawi ya njala. (1 Akorinto 16:1-4) Ofesi ya Mboni za Yehova ya m’deralo imasankha komiti yoti iyang’anire ndi kuyendetsa ntchito yothandiza anthuyo. Anthu a Mboni a m’madera ena amapereka chuma chawo kuti chithandizire pa ntchitoyo ndipo amadzipereka kuti agwire nawo ntchitoyo.—Miyambo 17:17.

Ndalama

Ndalama zimene anthu amapereka mwakufuna kwawo zimatumizidwa ku ofesi ya Mboni za Yehova. Zina mwa ndalama zimenezi zimagwiritsidwa ntchito pothandiza anthu amene akhudzidwa ndi tsoka. (Machitidwe 11:27-30; 2 Akorinto 8:13-15) Anthu onse amagwira ntchitoyo mongodzipereka ndipo zimenezi zimathandiza kuti ndalama zonse zigwire ntchito yothandiza anthu amene akhudzidwa ndi tsokalo osati kulipirira anthu ogwira ntchito. Timasamala kwambiri pogwiritsa ntchito zopereka.—2 Akorinto 8:20.