Pitani ku nkhani yake

N’chifukwa Chiyani Mumalalikira Kunyumba ndi Nyumba?

N’chifukwa Chiyani Mumalalikira Kunyumba ndi Nyumba?

 Yesu anauza otsatira ake kuti: “Pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira anga.” (Mateyu 28:19, 20) Pamene Yesu ankatumiza ophunzira ake oyambirira kuti akalalikire, anawauza kuti apite kunyumba za anthu. (Mateyu 10:7, 11-13) Yesu atamwalira, Akhristu oyambirira anapitiriza kulalikira uthenga wawo “poyera komanso kunyumba ndi nyumba.” (Machitidwe 5:42; 20:20) Ifenso timatsatira chitsanzo cha Akhristu oyambirira amenewo polalikira kunyumba ndi nyumba ndipo timaona kuti ndi njira yabwino kwambiri yopezera anthu.