Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

N’chifukwa Chiyani Mumakana Kuikidwa Magazi?

N’chifukwa Chiyani Mumakana Kuikidwa Magazi?

Maganizo olakwika amene anthu ena amakhala nawo

Zimene ena amanena: A Mboni za Yehova amakana chithandizo chilichonse chamankhwala.

Zoona zake: Timayesetsa kupeza chithandiza chabwino chamankhwala kuti ifeyo pamodzi ndi anthu a m’banja lathu tikhale anthu athanzi. Tikadwala, timapita kwa madokotala odziwa bwino ntchito yawo omwe amatha kupereka chithandizo chamankhwala kapena kuchita opaleshoni popanda kuika munthu magazi. Timayamikira kwambiri luso limene madokotala ali nalo masiku ano. Ndipotu njira yothandiza anthu popanda kuwaika magazi, yomwe madokotala anaitulukira n’cholinga choti azithandizira anthu a Mboni, tsopano ikugwiritsidwa ntchito pothandizanso anthu ena. M’mayiko ambiri, munthu aliyense amene akudwala angasankhe kukana kuti asaikidwe magazi n’kupewa mavuto ena monga matenda opatsirana kudzera m’magazi ndiponso mavuto ena.

Zimene ena amanena: A Mboni za Yehova amakhulupirira kuti munthu akadwala, akhoza kuchira ngati ali ndi chikhulupiriro.

Zoona zake: Ife sitikhulupirira machiritso kapena kuchiritsidwa chifukwa cha chikhulupiriro.

Zimene ena amanena: Njira zothandizira odwala popanda kuwaika magazi n’zokwera mtengo kwambiri.

Zoona zake: Njira zothandizira odwala popanda kuwaika magazi si zokwera mtengo. a

Zimene ena amanena: Anthu ambiri a Mboni, ndi ana omwe, amafa chaka chilichonse chifukwa chokana kuikidwa magazi.

Zoona zake: Limeneli ndi bodza lamkunkhuniza. Madokotala amachita maopaleshoni akuluakulu komanso ovuta kwambiri popanda kuika magazi wodwalayo. Mwachitsanzo, madokotala amatha kuchita maopaleshoni monga a mtima, a msana ndi mafupa ena ndiponso ochotsa kapena kuika ziwalo zina. b Odwala, kuphatikizapo ana, amene amathandizidwa popanda kuwaika magazi nthawi zambiri amachira msanga komanso zimawayendera bwino poyerekezera ndi odwala omwe aikidwa magazi. c Komanso tisaiwale mfundo yakuti palibe amene anganeneretu kuti wodwala angamwalire chifukwa choti wakana kuikidwa magazi. Palibenso anganeneretu kuti wodwala wina sangamwalire chifukwa choti wavomera kuikidwa magazi.

N’chifukwa chiyani a Mboni za Yehova amakana kuikidwa magazi?

Iyi ndi nkhani yokhudzana ndi kulambira Mulungu, osangoti yokhudzana ndi chithandizo cha mankhwala basi. M’Baibulo, ku Chipangano Chakale ndi Chatsopano chomwe, muli malamulo omveka bwino akuti tipewe magazi. (Genesis 9:4; Levitiko 17:10; Deuteronomo 12:23; Machitidwe 15:​28, 29) Komanso Mulungu amaona kuti magazi amaimira moyo. (Levitiko 17:14) Choncho timapewa magazi osati posonyeza kumvera Mulungu basi koma posonyeza kumulemekeza popeza ndi Mulunguyo amene amapereka moyo.

Anthu ena akusintha maganizo

N’zotheka kuchita maopaleshoni akuluakulu komanso ovuta kwambiri popanda kuika magazi anthu odwalawo

M’mbuyomo, madokotala ankaona kuti njira zothandizira odwala popanda kuwaika magazi zinali zoopsa kwambiri. Koma masiku ano, madokotala ambiri asintha maganizo amenewo. Mwachitsanzo, mu 2004 m’magazini inayake ya nkhani zachipatala munali nkhani imene inanena kuti “njira zambiri zimene zakonzedwa kuti tizithandizira anthu a Mboni za Yehova akadwala, m’tsogolo muno zidzalowa m’malo mwa njira zinazi ndipo tidzayamba kuzigwiritsa ntchito pothandizira anthu onse.” d M’chaka cha 2010, magazini inanso inati: “Njira yochitira opaleshoni popanda kuika wodwalayo magazi izigwiritsidwanso ntchito pothandiza odwala ena masiku ano, osati a Mboni za Yehova okha.”​—Heart, Lung and Circulation.

Madokotala ambirimbiri masiku ano akuthandiza odwala powachita maopaleshoni akuluakulu komanso ovuta koma popanda kuwaika magazi. Zimenezi zikuchitika ngakhale m’mayiko osauka ndipo odwala ambiri, omwe si a Mboni, akumapempha kuti awachite opaleshoni popanda kuwaika magazi.

a Onani buku lachingelezi lakuti, Transfusion and Apheresis Science, Voliyumu 33, Na. 3, tsa. 349.

b Onani mabuku achingelezi otsatirawa: The Journal of Thoracic and Cardiovascular Surgery, Volume 134, No. 2, pp. 287-288; Texas Heart Institute Journal, Volume 38, No. 5, p. 563; Basics of Blood Management, p. 2; and Continuing Education in Anaesthesia, Critical Care & Pain, Volume 4, No. 2, p. 39.

c Onani mabuku achingelezi otsatirawa: The Journal of Thoracic and Cardiovascular Surgery, Volume 89, No. 6, p. 918; and Heart, Lung and Circulation, Volume 19, p. 658.

d Continuing Education in Anaesthesia, Critical Care & Pain, Volume 4, No. 2, page 39.