Pitani ku nkhani yake

N’chifukwa Chiyani Malo Anu Opempherera Mumawatchula Kuti Nyumba ya Ufumu?

N’chifukwa Chiyani Malo Anu Opempherera Mumawatchula Kuti Nyumba ya Ufumu?

Dzinali ndi loyenera chifukwa:

  • Nyumbayo imakhala malo osonkhanira.

  • Timasonkhana kuti tilambire Yehova, yemwe ndi Mulungu wotchulidwa m’Baibulo, komanso kuti tichitire umboni za iye.—Salimo 83:18; Yesaya 43:12.

  • Timasonkhananso kuti tiphunzire za Ufumu wa Mulungu, umene Yesu ankakonda kuutchula.—Mateyu 6:9, 10; 24:14; Luka 4:43.

Ngati mungakonde mukhoza kudzasonkhana nawo mu Nyumba ya Ufumu imene muli nayo pafupi kuti mudzaone mmene a Mboni za Yehova amachitira misonkhano yawo.