Zechariah Wa wakhala ali m’ndende ku Singapore kuyambira mu August 2025
A Mboni za Yehova Anamangidwa Chifukwa cha Zimene Amakhulupirira—Potengera Dera
Pofika mu December 2025, a Mboni za Yehova oposa 261 padziko lonse anamangidwa chifukwa cha zimene amakhulupirira.
Gawo 18 la malamulo a padziko lonse okhudza ufulu wa anthu limanena kuti anthu ali ndi ufulu wa maganizo, chikhulupiriro komanso chipembedzo. Ngakhale zili choncho, a Mboni za Yehova m’mayiko ena sakupatsidwa ufulu umenewu ndipo amamangidwa komanso kuzunzidwa chifukwa cha zimene amakhulupirira kapena chifukwa chokana kulowa usilikali.
“Muzikumbukira amene ali mʼndende ngati kuti mwamangidwa nawo limodzi.”—Aheberi 13:3.

